Yes. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za munda wamphesa wa Chauta

1 Yob. 41.1; Mas. 74.14; 104.26 Tsiku limenelo Chauta adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, kulanga Leviyatani, chinjoka chothaŵa chija, Leviyatani njoka yozeŵezeka, ndipo adzaphanso chilombo choopsa cham'nyanja.

2Tsiku limenelo

Chauta adzalankhula za munda wake wokoma wamphesa.

Adzati,

3“Ine Chauta ndine mlonda wa mundawo,

nthaŵi zonse ndimauthirira.

Ndimaulonda usana ndi usiku,

kuti wina angauwononge.

4“Sindidzaukwiyiranso munda wanga wamphesawo.

Minga ndi mkandankhuku zidakati ziwoneke,

ndikadalimbana nazo ndi kuzitentha kotheratu.

5Koma ngati adani a anthu anga

afuna kuti ndiŵatchinjirize,

apangane nane za mtendere,

ndithu apangane nane za mtendere.”

6Masiku akudzawo, Yakobe adzazika mizu,

Israele adzachita mphukira ndi maluŵa.

Ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso zake.

7Kodi Chauta adalanga Aisraele monga

m'mene adalangira adani ao?

Kodi Aisraele adaphedwa monga m'mene adaphera adani ao?

8Chauta adaŵalanga pa kuŵapirikitsa

ndi kuŵatumiza ku ukapolo.

Adaŵachotsa ndi mpweya wake waukali,

monga momwe kumachitikira

pa tsiku la mkuntho wochokera kuvuma.

9Motero machimo a Israele adzakhululukidwa,

ndipo adzaonetsa kulapa kwathunthu,

akadzaphwanya miyala yonse ya maguwa

achikunja ndi kuisandutsa fumbi.

Maguwa ofukizapo lubani ndiponso

mafano ofanizira Asera sadzaonekanso.

10Mzinda wamalinga wasanduka bwinja.

Wasanduka malo osiyidwa ndi oiŵalika ngati chipululu.

Kumeneko kwasanduka busa la ziŵeto,

ndipo ziŵeto zimapumulako

ndi kumadya nthambi za mitengo.

11Nthambi za mitengoyo zikauma, amazithyola,

ndipo akazi amazitola nazisandutsa nkhuni.

Popeza kuti anthuŵa ndi osamvetsa,

nchifukwa chake Mulungu amene

adaŵalanga sadzaŵamvera chisoni,

Iye amene adaŵapanga sadzaŵachitira chifundo.

12Tsiku limenelo Chauta mwini wake adzasonkhanitsa anthu ake mmodzimmodzi, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Ejipito.

13Tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira kuitana Aisraele onse amene adaali mu ukapolo ku Asiriya ndi ku Ejipito. Iwowo adzabwera, ndipo adzapembedza Chauta pa phiri lake loyera la ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help