Yer. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za madengu aŵiri a nkhuyu

1 mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu. Adaatenganso ukapolo akalonga onse a ku Yuda, anthu aluso ndi akatswiri enanso kupita nawo ku Babiloni. Nthaŵi imeneyo Chauta adandiwonetsa zinthu zina m'masomphenya, zinthuzo ndi izi: ndidaona madengu aŵiri a nkhuyu ali pakhomo pa Nyumba ya Chauta.

2M'dengu lina munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma m'dengu linalo munali nkhuyu zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.

3Chauta adandifunsa kuti, “Iwe Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nkhuyu zabwino kwambiri, ndi zinanso zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.”

4Tsono Chauta adandiwuza kuti,

5“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Akapolo a ku Yuda amene ndidaŵachotsa ku malo ano, kupita nawo ku dziko la Ababiloni, ndikuŵafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.

6Ndidzachita chotheka kuti ndiŵachitire zabwino ndi kuŵabwezeranso ku dziko lao. Ndidzaŵamanga osati kuŵapasula. Ndidzaŵakhazikitsa, osati kuŵazula ai.

7Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse.

8“Koma monga nkhuyu zoipa zija, zosatinso kudyekazi, ndimo m'mene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi akalonga, ndi onse otsala a mu Yerusalemu amene ali m'dziko lino, ndiponso Ayuda amene akukhala m'dziko la Ejipito.

9Ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi, chinthu chonyozeka, chinthu chopanda pake, chinthu chomachiseka ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzaŵapirikitsire.

10Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka onsewo nditaŵapululiratu m'dziko limene ndidaŵapatsa iwowo ndi makolo ao.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help