1 Mt. 5.34; 23.22; Mt. 5.35 Ntc. 7.49, 50 Chauta akunena kuti,
“Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu,
dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga.
Kodi ndi nyumba yotani
imene mungathe kundimangira inu?
Ndi malo otani amene inu mungandikonzere
kuti Ine ndizipumulirapo?
2Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine,
tsono zonsezi nzanga,”
akutero Chauta.
“Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa:
odzichepetsa ndi olapa,
ondiwopa ndi omvera mau anga.
3“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera.
Kwa iwo nchimodzimodzi
kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe
kapena kupha munthu,
kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe
kapena kupha galu,
kupereka chopereka cha chakudya
kapena kupereka magazi a nkhumba,
kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso
kapena kupembedza fano.
Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.
4Ine tsono ndidzaŵagwetsera chilango
ndipo ndidzaŵachititsa mantha,
chifukwa nditaŵaitana, palibe amene adandiyankha,
kapena kutchera khutu pamene ndinkalankhula.
Adachita zoipa pamaso panga,
adasankhula kuchita zimene zimandinyansa.”
5Imvani mau a Chauta,
inu amene mumanjenjemera akamalankhula.
Iye akuti, “Abale anu omwe amene amadana
nanu nakukanani chifukwa cha dzina langa,
amati, ‘Chauta alemekezeke,
kuti ife tiwone chimwemwe chanu.’
Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
6“Imvani mfuu mu mzinda!
Imvani liwu m'Nyumba ya Mulungu,
liwu la Chauta amene akulanga adani ake.
7 Chiv. 12.5 “Mzinda wangawu uli ngati mai
amene akubadwitsa mwana
asanayambe kumva zoŵaŵa zake,
amene akubala mwana wamwamuna
kupweteka kusanayambike.
8Ndani adamvapo zoterezi?
Ndani adaziwonapo zoterezi?
Kodi dziko nkupangika tsiku limodzi?
Kodi mtundu wa anthu nkubadwa tsiku limodzi?
Koma Ziyoni adabala ana ake aamuna,
atangoyamba kuvutika kumene.
9Kodi ine ndidzafikitsa anthu anga
mpaka nthaŵi yobala,
koma osalola kuti abaledi?”
Akuterotu Chauta.
“Kodi Ine, amene ndili wobalitsa,
ndingatseke mimba nthaŵi imeneyo?”
Akuterotu Mulungu wako.
10“Kondwera nayeni Yerusalemu,
musangalale chifukwa cha iye,
inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu.
Kondwera nayeni mwachimwemwe,
nonsenu amene mukumlira.
11Mudzalandira chitonthozo ndi
kukondwera nacho kwambiri.
Mudzagaŵana naye ulemerero wake
ndi kusangalala nawo.”
12Chauta akunena kuti,
“Ndidzakupatsa zabwino zochuluka
ngati mtsinje wa madzi.
Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu
ngati mtsinje wosefukira.
Mudzakhala ngati mwana woyamwa
amene mai wake wamnyamulira pambalipa,
kapena akumluluza pa maondo.
13Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu
monga momwe mai amasangalatsira mwana wake.
14Mudzasangalala poona zimenezi.
Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu.
Tsono mudzadziŵa kuti Ine Chauta
ndimathandiza amene amandimvera,
ndipo ndimakwiyira adani anga.”
15“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto.
Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho.
Iye adzaonetsa poyera ukali wake,
ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto.
16Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi
ndi moto ndi lupanga.
Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”
17Chauta akunena kuti, “Amene akuti akudzipatula ndi kudziyeretsa pamene akufuna kuchita miyambo yam'minda ija, ali ndi mtsogoleri wao yemwe, nkumadya nyama yankhumba, mbeŵa ndi zonyansa zina, onsewo adzafera limodzi,” akuterotu Chauta.
18“Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga.
19“Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzaŵatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi a ku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso ku Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuwona ulemerero wanga. Iwowo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
20Ndipo adzabwera nawo abale anu onse kuchokera kwa anthu a mitundu yonse, kuti akhale mphatso kwa Ine. Adzabwera nawo ku phiri langa loyera la Yerusalemu, abale anuwo ataŵakweza pa akavalo, abulu, ngamira ndiponso pa magaleta ndi ngolo. Adzabwera nawo monga momwe Aisraele amabwerera ndi zopereka za chakudya ku Nyumba ya Mulungu, atazitenga m'ziŵiya zotsukatsuka,
21ndipo ena mwa iwo ndidzaŵasandutsa ansembe ndi Alevi,” akutero Chauta.
22 Yes. 65.17; 2Pet. 3.13; Chiv. 21.1 “Monga momwe dziko lapansi latsopano
ndi dziko lakumwamba latsopano,
zimene ndidzapange,
zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga,
chonchonso zidzukulu zanu ndi dzina lanu
zidzakhala mpaka muyaya.
23Anthu a mitundu yonse adzabwera
kudzandipembedza ku Yerusalemu,
pa chikondwerero chilichonse cha pokhala mwezi,
ndi tsiku la Sabata lililonse,”
akutero Chauta.
24 Yud. 16.17; Mk. 9.48 “Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.