1 2Maf. 4.8-37 Ndiye kuti Elisa anali atauza mai amene adaamuukitsira mwana wake uja kuti, “Nyamuka upite pamodzi ndi a pabanja pako, ukakhale nawo kulikonse kumene ungathe kukakhala, pakuti Chauta akubweretsa pa dziko njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri.”
2Motero maiyo adanyamuka, ndipo adachitadi monga momwe munthu wa Mulungu uja adaanenera. Adapita pamodzi ndi a pabanja pake, nakakhala nawo ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziŵiri.
3Tsono zitatha zaka zisanu ndi ziŵirizo, mai uja adabwerako ku dziko la Afilisti kuja, ndipo adapitanso kwa mfumu ya ku Israele kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.
4Atafika kwa mfumu, adapeza mfumuyo ikulankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu uja, nimafunsa kuti, “Tandiwuza zonse zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
5Pamene mtumikiyo ankauza mfumuyo m'mene Elisa adaukitsira anthu akufa, mkazi uja, amene mwana wake Elisa adamuukitsira, adadzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Pamenepo Gehazi adati, “Inu mbuyanga mfumu, pano pali mai, ndipo mwana wake ndi uyu amene Elisa adamuukitsa.”
6Mfumu itamufunsa maiyo, iyeyo adaifotokozera kuti Elisa adaukitsadi mwana wake. Choncho mfumu ija idamuikira nduna maiyo niiwuza kuti, “Umbwezere zonse zimene zidaali zake, pamodzi ndi phindu lonse lochokera ku zokolola za kumunda kwake, kuyambira tsiku limene adachoka mpaka tsopano lino.”
Elisa ndi mfumu Benihadadi wa ku Siriya7Tsiku lina Elisa adapita ku Damasiko, pa nthaŵi imene Benihadadi mfumu ya ku Siriya ankadwala. Mfumuyo itamva kuti kwabwera munthu wa Mulungu,
8idauza Hazaele nduna yake yaikulu kuti, “Tenga mphatso, upite kukakumana naye munthu wa Mulunguyo. Tsono upemphe nzeru kwa Chauta kudzera mwa iyeyo kuti, ‘Kodi mfumu idzachira matenda ameneŵa?’ ”
9Motero Hazaele adapita kukakumana ndi mneneri Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso ndi zinthu zokoma zosiyanasiyana za ku Damasiko. Atafika, adakaima pamaso pa Elisa, munthu wa Mulungu uja, nati, “Munthu wanu Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, wandituma kuti ndikufunseni kuti, kodi ati adzachira?”
10Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti adzafa, komabe pita ukamuuze kuti adzachira.”
11Atatero, Elisa adamuyang'ana kwambiri Hazaele mpaka adachita manyazi. Apo Elisayo adayamba kulira.
12Tsono Hazaele adamufunsa kuti, “Mbuyanga, mukuliranji?” Iyeyo adayankha kuti, “Chifukwa ndikudziŵa zoipa zimene mudzaŵachita Aisraele. Mudzatentha malinga ao ankhondo ndipo mudzapha ankhondo ao ambiri. Mudzapondereza tiana tao, ndipo mudzang'amba akazi ao apakati.”
131Maf. 19.15 Apo Hazaele adafunsa kuti, “Kodi kapolo wanune amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita zinthu zazikulu zoterezi?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Asiriya.”
14Pomwepo Hazaeleyo adasiyana naye Elisa, napita kwa mbuyake. Mbuyakeyo adamufunsa kuti, “Kodi Elisa wakuuza zotani?” Hazaele adayankha kuti, “Inuyo muchira ndithu.”
15Koma m'maŵa mwake, Hazaele adatenga chofunda nachiviika m'madzi nkuchiphimba kumaso kwa mfumu, ndipo mfumu ija idafa. Motero Hazaele adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Yehoramu mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 21.1-20)16Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, Yehoramu, mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adayambapo kulamulira dziko la Yuda.
17Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.
18Tsono Yehoramuyo ankatsata makhalidwe oipa a mafumu a ku Aisraele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zili zonse pamaso pa Chauta.
191Maf. 11.36 Komabe Chauta sadafune kuwononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake, popeza kuti Chauta adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
20 Gen. 27.40 Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda ndipo adadzisankhira mfumu yao.
21Tsono Yehoramu adapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse ankhondo. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake. Ankhondo ake onse adathawa napita kwao.
22Motero Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wake.
23Tsono ntchito zina za Yehoramu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
24Choncho Yehoramu adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Ahaziya mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 22.1-6)25Pa chaka cha 12 cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya ku Israele, Ahaziya mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira.
26Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri mfumu ya ku Israele.
27Iyeyonso ankatsata chitsanzo choipa cha banja la Ahabu. Adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, poti anali mkamwini m'banja la Ahabu lomwelo.
28Tsono mfumu Ahaziya adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adalasa Yoramu.
29Tsono Yoramuyo adabwerera napita ku Yezireele, kuti akamchiritse mabala amene Asiriya adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.