Mas. 34 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yotamanda ubwino wa MulunguSalmo la Davide. Anali atanyengezera kukhala ngati wamisala pamaso pa Abimeleki. Pamenepo nkuti Abimelekiyo atapirikitsa Davide.

1Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse,

pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza.

2Moyo wanga umanyadira Chauta.

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

3Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta,

tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.

4Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha.

Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.

5Ozunzikawo atayang'ana kwa Chauta,

nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi.

6Munthu wosaukayu adalira,

ndipo Chauta adamumva,

nampulumutsa m'mavuto ake onse.

7Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye,

ndipo amaŵapulumutsa.

8 1Pet. 2.3 Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta.

9Muzimvera Chauta, inu anthu ake oyera mtima,

pakuti amene amamumvera sasoŵa kanthu.

10Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya

ndipo amakhala anjala,

koma anthu amene amalakalaka Chauta,

sasoŵa zinthu zabwino.

11Bwerani ana anga, mundimvere,

ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.

12 1Pet. 3.10-12 Ndani mwa inu amakhumba moyo

ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri,

kuti asangalale ndi zinthu zabwino?

13Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa,

pakamwa pako pasakambe zonyenga.

14Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino.

Funafuna mtendere ndi kuulondola.

15Ngati mumvera Chauta,

adzakuyang'anirani

ndipo adzayankha kupempha kwanu.

16Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa,

anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano.

17Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize,

Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.

18Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka,

amapulumutsa otaya mtima.

19Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri.

Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.

20 Yoh. 19.36 Chauta amasunga thupi la munthuyo,

palibe fupa limene limasweka.

21Choipa chitsata mwini,

anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa.

22Chauta amaombola moyo wa atumiki ake.

Palibe wothaŵira kwa Iye

amene adzalangidwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help