1 Aro. 3.18 Uchimo umalankhula
mu mtima wa munthu wosamvera Mulungu.
Alibe mantha ndi Mulungu m'maganizo mwake.
2Amadzinyenga m'maganizo mwake,
kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira
ndi kudana nalo.
3Mau a pakamwa pake ndi oipa ndi onyenga.
Sachita zanzeru kapena zabwino.
4Amaganiza zachiwembu akamagona usiku.
Amayenda pa njira imene siili yabwino,
sapewa zoipa.
Za ubwino wa Mulungu.5Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika
chimafika mpaka kumwamba,
kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
6Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali,
kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya,
Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
7Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali.
Nchifukwa chake anthu anu
amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
8Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu,
ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu.
9Kwa Inu kuli kasupe wamoyodi,
m'kuŵala kwanu ifenso timaona kuŵala.
10Musaleke kuŵakonda ndi chikondi chanu chosasinthika
anthu okudziŵani,
pitirizani kuŵachitira zokoma
anthu olungama mtima.
11Musalole kuti mapazi a anthu odzikuza andipondereze,
ndipo kuti manja a anthu oipa andipirikitse.
12Onani, ochita zoipa ali ngundangunda.
Inu mwaŵagwetsa pansi ndipo sangathe kudzuka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.