1Ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense adatenga chofukizira lubani naikamo makala amoto. Pamakalapo adathirapo lubani, ndipo adapereka kwa Chauta moto umene Iye sadalamule.
2Tsono Chauta adatumiza moto nuŵapsereza, ndipo onsewo adafa pamaso pa Chauta.
3Apo Mose adauza Aroni kuti, “Pajatu Chauta adanena kuti, ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga kwa onse amene ali pafupi ndi Ine, ndipo ndidzalemekezedwa pamaso pa anthu onse.’ ” Koma Aroni adakhala chete osalankhula.
4Mose adaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, bambo wamng'ono wa Aroni, naŵauza kuti, “Senderani pafupi, achotseni abale anuŵa pa malo oyera ndipo muŵatulutsire kunja kwa mahema.”
5Iwo adasenderadi pafupi, naŵanyamula ali ndi mikanjo yao ndi kuŵatulutsira kunja kwa mahema, monga momwe Mose adaŵauzira.
6Tsono Mose adauza Aroni ndi ana ake Eleazara ndi Itamara kuti, “Musalilekerere tsitsi lanu, ndipo musang'ambe zovala zanu, kuti mungafe, ndiponso kuti mkwiyo ungagwere mpingo wonse. Koma abale anu a m'fuko lonse la Israele ndiwo alire chifukwa cha imfa ya moto umene Chauta watentha nawo anzanu.
7Musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano kuti mungafe, chifukwa mudadzozedwa ndi mafuta a Chauta.” Iwo adachita monga momwe Mose adanenera.
Malamulo okhudza ansembe8Tsono Chauta adalankhula ndi Aroni namuuza kuti,
9“Usamwe vinyo kapena chakumwa china champhamvu, iwe ndi ana ako uli nawoŵa, pamene mukupita ku chihema chamsonkhano, kuwopa kuti mungafe. Limeneli likhale lamulo losatha pa mibadwo yanu yonse.
10Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zonyansa ndi zinthu zoyenera pa zachipembedzo.
11Muŵaphunzitse Aisraele malamulo onse amene Chauta adapereka kudzera mwa Mose.”
12 Lev. 6.14-18 Mose adauza Aroni ndi ana ake otsalira aja, Eleazara ndi Itamara, kuti, “Tengani zopereka za zakudya zimene zatsalako pa nsembe yotentha pa moto ija, yopereka kwa Chauta, ndipo muzidye zosafufumitsa pafupi pa guwa, pakuti zimenezi nzopatulika kopambana.
13Muzidye pa malo oyera, chifukwa zimenezi ndakugaŵiraniko kuchokera pa nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta, kuti zikhale zanu, iwe ndi ana ako. Ndithudi, zimenezi ndizo zimene Chauta adandilamula.
14Lev. 7.30-34 Koma nganga yopereka moweyula manja ija, pamodzi ndi ntchafu yopereka, muzidyere pa malo aliwonse oyenera pa zachipembedzo, iweyo ndi ana ako aamuna ndi aakazi amene ali nawe. Zimenezi zapatsidwa kwa iwe kuti zikhale zako ndi za ana ako, kuchokera pa nsembe yachiyanjano imene aipereka Aisraele.
15Ntchafu yoperekayo ndi nganga yoweyulayo, abwere nazo pamodzi ndi zopereka za nsembe yamafuta yotentha pa moto, ndipo uziweyule, kuti zikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi zikhale zako ndi za ana ako aamuna uli nawoŵa mpaka muyaya, monga momwe Chauta adaalamulira.”
16Tsono Mose adafunafuna mbuzi ya nsembe yopepesera machimo, ndipo adapeza kuti adaitentha kale. Ndipo adakalipira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni otsala aja. Adati,
17Lev. 6.24-26 “Chifukwa chiyani simudadyere pa malo oyera nsembe yopepesera machimo ija? Kodi si yopatulika kwambiri? Kodi siyoperekedwa kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse, kuti muŵachitire mwambo wopepesera machimo ao pamaso pa Chauta?
18Chifukwa magazi ake sadaloŵe nawo m'katikati mwa malo oyera kwambiri, mukadayenera kudyera zimenezi pa malo oyera, monga momwe ndidalamulira.”
19Ndipo Aroni adauza Mose kuti, “Taonani, lero anthu apereka nsembe yao yopepesera machimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Chauta. Komabe zinthu zoopsa zoterezi zandigwera ine. Nanga ndikadadya zopereka za nsembe yopepesera machimo lero, kodi Chauta akadakondwa?”
20Mose atamva zimenezo, adakhutira nazo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.