Owe. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mika ndi fuko la Dani.

1Masiku amenewo kunalibe mfumu ku dziko la Israele. Anthu a fuko la Dani ankafunafuna dziko loti azikhalamo, kuti likhale choloŵa chao, pakuti mpaka nthaŵi imeneyo nkuti iwowo asanalandire choloŵa pakati pa mafuko a Aisraele.

2Choncho anthu a fuko la Daniwo adatuma anthu asanu olimba mtima, osankhidwa mwa mabanja ao onse. Anthuwo adachokera ku Zora ndi ku Esitaoli, adatumidwa kuti akazonde dziko ndi kuliyendera. Anthu onse adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dzikolo.” Iwowo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika, nagona komweko.

3Ali kunyumba kumeneko, adazindikira liwu la mnyamata wachilevi uja ndipo adapita kwa iye nakamufunsa kuti, “Udabwera ndi yani kuno? Ukuchita chiyani kuno? Ukugwira ntchito yanji kuno?”

4Iyeyo adaŵauza kuti, “Ndili pa chipangano ndi Mika, adandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.”

5Iwo aja adamuuza kuti, “Chonde, tatifunsirako kwa Mulungu, kuti tidziŵe ngati ulendo wathu uno tiyende bwino.”

6Wansembeyo adaŵauza kuti, “Pitani ndi mtendere. Ulendo wanuwu Chauta akuuyang'anira.”

7Apo anthu asanu aja adachoka nakafika ku Laisi. Adakaona anthu amene ankakhala kumeneko, nazindikira kuti anthuwo ankakhala popanda choŵavuta, monga momwe ankakhalira Asidoni. Anali anthu aphee ndi opanda tcheru, osasoŵa kanthu kalikonse ndiponso anali anthu achuma. Adaona kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Asidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena.

8Okazonda dziko aja atabwerera kwa abale ao ku Zora ndi ku Esitaoli, abale aowo adaŵafunsa kuti, “Nanga mutisimbira zotani?”

9Iwo adayankha kuti, “Fulumirani, tiyeni tikamenyane nawo nkhondo, pakuti dziko laolo taliwona, nlachonde kwambiri. Monga inu simuchitapo kanthu? Musachedwe kukaloŵa m'dzikomo ndi kukalilanda.

10Mukapita, mukaŵapeza kuti ndi anthu opanda tcheru. Dzikolo nlalikulu. Ndithudi Mulungu walipereka m'manja mwanu dziko limenelo. Malowo ngosasoŵa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.”

11Tsono anthu 600 a fuko la Dani adatenga zida zankhondo, nanyamuka ku Zora ndi ku Esitaoli.

12Adakamanga zithando zankhondo ku Kiriyati-Yearimu m'dziko la Yuda. Chifukwa cha chimenechi malowo akutchedwa zithando za Dani mpaka pano, ndipo ali kuzambwe kwa Kiriyati-Yearimu.

13Kuchokera kumeneko adapita ku dziko lamapiri la ku Efuremu, nakafika ku nyumba ya Mika.

14Tsono anthu asanu amene adaapita kukazonda dziko la Laisi aja adaŵafunsa abale aowo kuti, “Kodi mukudziŵa kuti imodzi mwa nyumba zimenezi muli chovala cha efodi, mafano am'nyumba, otchedwa terafimu, ndiponso fano losema ndi lina lachitsulo? Ndiye mudziŵa chochita.”

15Anthuwo adapatuka nakafika kunyumba kwa Mika, kumene mnyamata wachilevi uja ankakhala, nakamufunsa m'mene zinkamuyendera zinthu.

16Nthaŵi imeneyo nkuti anthu 600 a fuko la Dani okhala ndi zida zankhondo aja ataima pa khomo lapachipata.

17Apo anthu asanu amene adaali atazonda dziko aja adakaloŵa nakatenga fano losema lija, chovala cha efodi, mafano am'nyumba aja, ndi fano lachitsulo. M'menemo nkuti wansembe ataimirira pa khomo lapachipata pamodzi ndi anthu 600 okhala ndi zida zankhondo aja.

18Pamene anthuwo adakaloŵa m'nyumba ya Mika ndi kukatenga fano losema lija, chovala cha efodi, mafano am'nyumba ndi fano lachitsulo, wansembeyo adaŵafunsa kuti, “Kodi chikatere, ndiye kuti chiyani?”

19Iwo adamuyankha kuti, “Khala chete, usalankhule, tiye kuno, ukakhale mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino koposa kwa iwe kuti ukhale wansembe wa fuko lathunthu la Israele m'malo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?”

20Apo mtima wake wa wansembeyo udasangalala, ndipo adatenga chovala cha efodi, mafano am'nyumba, ndi fano losema lija, natsagana nawo anthuwo.

21Choncho adachoka napita, atatsogoza ana, ng'ombe ndiponso akatundu ao.

22Atapita kamtunda ndithu kuchokera pa nyumba ya Mika, Mikayo ndi anthu amene anali m'nyumba zoyandikana naye, adasonkhana kuti alondole anthu a fuko la Dani ndipo adaŵapeza.

23Iwowo adafuulira anthu a fuko la Dani aja ndipo anthu a fuko la Daniwo adatembenukira kumbuyo nafunsa Mika kuti, “Kodi chakuvuta nchiyani kuti uzibwera ndi chigulu chotere?”

24Mika adaŵayankha kuti, “Mwanditengera milungu yanga imene ine ndidapanga, mwandilandanso wansembe wanga nkumapita, nanga ine chanditsalira nchiyani? Ndiye inu mungandifunse kuti, ‘Kodi chakuvuta nchiyani?’ ”

25Anthu a fuko la Dani aja adayankha kuti, “Usaonjezenso mau ena, mwinamwina anthu aŵa apsa mtima nakumenya, ndipo iweyo ndi banja lako nonse muphedwa.”

26Tsono anthu a fuko la Dani aja adapita, ndipo pamene Mika adaona kuti anthuwo ngamphamvu kupambana iyeyo, adangobwerera kunyumba kwake.

27Atatenga zinthu zimene Mika adapanga zija pamodzi ndi wansembe wake uja, anthu a fuko la Daniwo adakafika ku Laisi kwa anthu aphee ndi opanda tcheru aja. Adaŵathira nkhondo naŵapha, nkutentha mzinda wao ndi moto.

28Kunalibe oŵapulumutsa, popeza kuti kunali kutali ndi ku Sidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena. Mzindawo unali m'chigwa cha ku Beterehobu. Anthu a fuko la Daniwo adamanganso mzindawo ndi kumakhalamo.

29Mzindawo adautcha Dani kutengera dzina la Dani kholo lao, amene anali mwana wa Israele. Koma dzina la mzindawo poyamba lidaali Laisi.

30Tsono anthu a fuko la Dani aja adaimiritsa fano la siliva wosungunula lija. Ndipo Yonatani, mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake onse, adakhala ansembe a anthu a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo.

31Motero anthu a fuko la Dani aja ankapembedza fano lija limene Mika adapanga, nthaŵi yonse pamene chihema cha Mulungu chinali ku Silo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help