1 Gen. 22.22 Tsono Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu pa phiri la Moriya, pamene Chauta adaaonekera Davide bambo wake, pa malo omwe Davide adaaloza, pa bwalo lopunthira tirigu la Orinani Myebusi.
2Solomoniyo adayamba kumanga pa mwezi wachiŵiri wa chaka chachinai cha ufumu wake.
3Nyumba ya Chautayo, miyeso yake imene Solomoni adaapereka inali iyi: Potsata miyeso yakale, m'litali mwake inali ya mamita 27, ndipo m'mimba mwake inali ya mamita asanu ndi anai.
4Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni.
5Chipinda chachikulucho adachichinga ndi matabwa amlombwa, nachikuta ndi golide wosalala, ndipo pamakoma adalochapo zithunzi za kanjedza ndi za maunyolo.
6Adaikometsa nyumbayo ndi miyala yamtengowapatali. Golide wake anali wa ku Paravaimu.
7Motero adaikuta nyumba yonseyo ndi golide, ndiye kuti mitanda yake, ziwundo zake, makoma ake ndi zitseko zake zomwe. Ndipo adazokota zithunzi za akerubi pa makoma.
8 Eks. 26.33, 34 Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri.
9Magaramu 570 a golide adaŵagwiritsa ntchito kupanga misomali. Ndipo zipinda zapamwamba adazikutanso ndi golide.
10 Eks. 25.18-20 Ku malo opatulika kwambiriko adapangako akerubi aŵiri achitsulo, ndipo adaŵakuta ndi golide.
11Mapiko a akerubiwo akaŵatambasula, pamodzi ankakwanira mamita asanu ndi anai. Phiko limodzi la kerubi mmodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba. Phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.
12Ndipo Kerubi ameneyu phiko lake limodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba, phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, lidalumikizana ndi phiko la kerubi woyamba uja.
13Mapiko a akerubi amenewo onse pamodzi akaŵatambasula ankakwanira mamita asanu ndi anai. Akerubiwo adaaimirira pa mapazi ao, kuyang'ana m'kati mwa nyumbayo.
14Eks. 26.31 Ndipo Solomoni adatenga nsalu yobiriŵira, ina yofiira, ina yofiirira, ndi bafuta wosalala, napangira nsalu yochingira, kenaka adapetapo zithunzi za akerubi.
Nsanamira ziŵiri zija zamkuŵa(1 Maf. 7.15-22)15Kumaso kwake kwa nyumbayo adamangako nsanamira ziŵiri za msinkhu wa mamita 15 ndi theka. Nsanamira iliyonse inali ndi mutu wa mamita aŵiri nkanthu pamwamba pake.
16Adapanga maunyolo okometsera, ofanafana ndi aja a m'kati mwa Nyumba ya Chauta, naŵaika pamwamba pa nsanamirazo. Adapanganso zinthu zonga makangaza zokwanira 100, ndipo adaziika ku maunyolowo.
17Adamanga nsanamirazo kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, ina chakumpoto. Yakumwerayo adaitchula kuti Yakini, yakumpotoyo Bowazi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.