1Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.
2Mt. 17.20; 21.21; Mk. 11.23Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse.
3Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.
4Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.
5Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
6Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona.
7Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
8Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.
9Paja timangodziŵa zinthu mopereŵera, ndipo kulalika kwathunso nkopereŵera,
10koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha.
11Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo.
12Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.
13Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.