Mphu. 37 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za abwenzi onyenga

1Bwenzi aliyense amati, “Inenso ndine bwenzi lako.”

Koma ena ndi abwenzi dzina chabe.

2Kodi si chinthu chomvetsa chisoni kwambiri

kuti mnzako kapena bwenzi lako asanduke mdani wako?

3Kodi zidachitika bwanji

kuti pendekero loipa chotere lidzaze dziko lapansi

ndi kunyenga anthu?

4Mnzako wina amakhala nawe mosangalala,

pamene uli pabwino,

koma pa nthaŵi ya mavuto amakupandukira.

5Mnzako weniweni amakuthandiza polimbana ndi adani ako,

nkhondo ikabuka, amatenga zida nkukuteteza.

6Usaiŵale bwenzi lako mumtima mwako,

usamtaye utalemera.

Za alangizi

7Mlangizi aliyense amakonda kupereka malangizo,

koma ena amangofunako phindu lao.

8Uchenjere naye munthu wodzakulangiza,

uyambe waona kuti akufunapo phindu lanji,

chifukwatu ameneyo makamaka akuganiza za iye

yemwe poyamba,

chilipo ndithu chimene wakukonzekera.

9Angathe kunena kuti;

“Zimene ukuchitazi ndi zabwino,”

namadikira kuti zinthu zikugwere.

10Usakapemphe nzeru kwa munthu amene amakupenekera,

usaulule zolinga zako kwa amene amakuchitira nsanje.

11Usafunse munthu wamkazi za amene amapikisana naye,

kapena munthu wamantha kumfunsa za nkhondo,

munthu wogulitsa kumfunsa za malonda,

munthu wogula kumfunsa za kugulitsa,

munthu waumbombo kumfunsa za kuthokoza,

munthu wouma mtima kumfunsa zachifundo,

munthu waulesi kumfunsa za ntchito ina iliyonse,

munthu waganyu kumfunsa za kutsiriza ntchito,

kapitao waulesi kumfunsa za ntchito yovuta.

Pofuna kupempha nzeru usadalire anthu ameneŵa.

12Koma iwe uziyendera munthu woopa Mulungu,

amene ukudziŵa kuti amatsata Malamulo,

amene amaganiza monga iwe,

amene adzakuthuzitsa mtima ukalakwa pena.

13Komanso udzifunsitse mtima,

chifukwa palibenso wina wokhulupirika ngati mtima wako.

14Nthaŵi zina mtima wa munthu umamudziŵitsa zambiri

kupambana alonda asanu ndi aŵiri okhala pa nsanja.

15Koma koposa zonsezo, uzipemphera

kwa Mulungu Wopambanazonse

kuti akuyendetse m'njira yoona.

16Ntchito iliyonse imayamba ndi kuganiza kwanzeru,

ndipo chilichonse choti uchite, uyambe

wachisinkhasinkha bwino.

17Maganizo mizu yake ili mu mtima.

18Mumtima mumaphuka nthambi zinai:

zabwino ndi zoipa, moyo ndi imfa.

Zonsezi mfumu yao ndi lilime.

19Munthu angathe kukhala ndi nzeru zophunzitsa ena,

koma iyeyo osatha kudzichitira kanthu kaphindu.

20Munthu wochenjera pakamwa anzake nkudana naye,

ndiye potsiriza pake amafa ndi njala.

21Zimenezi zimachitika

chifukwa Ambuye sadamukomere mtima,

ndipo iyeyo alibe nzeru.

22Wina amadziyesa wochenjera,

koma zimene amaphunzitsa

zimakhala zoona kwa iye yekha.

23Munthu waluntha weniweni

amaphunzitsa anthu ake,

zimene amaphunzitsa

zimakhala zoona ndithu kwa aliyense.

24Munthu wanzeru anthu amamtamanda,

onse omuwona amamutcha wodala.

25Masiku a moyo wa munthu ngoŵerengeka,

koma masiku a moyo wa Israele ngosaŵerengeka.

26Munthu wanzeru anthu onse amamkhulupirira,

ndipo adzamkumbukira nthaŵi zonse.

Za kudziletsa

27Mwana wanga, pa moyo wako wonse uzidziyesayesa.

Zindikira bwino zimene zili zoipa kwa iwe ndipo usazilole.

28Chifukwa si zonse zimakhalira bwino

munthu aliyense,

ndipo si munthu aliyense amakondwera

ndi zinthu zonse.

29Usachite khwinthi ndi tokomera m'kamwa,

usakhale wadyera pa chakudya.

30Munthu akakhutitsa amadwala,

kudyetsa kwambiri kumachititsa ntchofu.

31Ambiri amafa chifukwa cha kudyetsa.

Ulewe zimenezi

ndipo udzakhala moyo nthaŵi yaitali.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help