Yer. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chauta akunena kuti, “Pa nthaŵi imeneyo anthu adzatulutsa m'manda mafupa a akalonga, a ansembe, a aneneri ndiponso a anthu onse amene ankakhala ku Yerusalemu.

2Adzaŵamwaza pa mtunda kuyang'ana mwezi, ndi nyenyezi zonse zakumwamba zimene ankazikonda, kumazitumikira, kuzitsata, kuzipempha nzeru ndi kumazipembedza. Mafupa amenewo sadzaŵasonkhanitsa kapena kuŵakwirira, koma adzasanduka ndoŵe pamwamba pa nthaka.

3Anthu onse otsala mwa anthu a mtundu woipawu, kulikonse kumene ndaŵapirikitsira, adzakonda kufa kupambana kuti akhale ndi moyo,” akuterotu Chauta Wamphamvuzonse.

Za uchimo ndi chilango chake

4Chauta adandiwuza

kuti ndifunse anthu ake mau aŵa:

“Kodi anthu akagwa, ndiye kuti sangathe kudzukanso?

Kodi munthu akasokera, ndiye kuti sangathe kubwereranso?

5Chifukwa chiyani nanga anthu ameneŵa

akupitirirabe kulakwa, osabwereranso?

Akangamira ndithu machimo ao,

akukana kubwerera.

6Ndakhala ndikutchereza ndi kuŵamvetsera,

koma sadalankhulepo zoona.

Palibe wochimwa aliyense

amene adandiwonetsa kuti walapa,

namanena kuti, ‘Ndachitanji ine?’

Koma aliyense akungotsata njira zake,

ngati kavalo wothamangira nkhondo.

7Mbalame amati kapande ija

imadziŵa nthaŵi yake mumlengalenga.

Nkhunda, namzeze ndi ngalu

zimadziŵa nthaŵi yake yonyamukira ulendo.

Koma anthu anga sadziŵa malangizo a Chauta.

8“Mungathe kunena bwanji kuti,

‘Ndife anzeru, timasunga malamulo a Chauta,

pamene alembi akulemba zabodza?’

9Anthu anzeru adzachita manyazi,

adzatha nzeru, ndipo adzagwidwa.

Akana mau a Chauta,

nanga nzeru zao nzotani?

10Nchifukwa chake akazi ao ndidzaŵapatsa kwa anthu ena,

minda yao ndidzaipereka kwa amene aŵagonjetsa.

Ndithudi, kuyambira ana ndi akulu omwe,

onsewo ali ndi khwinthi la phindu lopeza monyenga.

Aneneri ndi ansembe omwe, onsewo ndi onyenga.

11 kulibe mankhwala ochiritsa?

Kodi kumeneko kulibe sing'anga?

Chifukwa chiyani mabala a anthu anga sadapole?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help