1 Ntc. 17.1 Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu.
Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Za moyo wa Atesalonika ndi chikhulupiriro chao2Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu.
3Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
4Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziŵa kuti Iye adakusankhani kuti mukhale ake.
5Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.
6 Ntc. 17.5-9 Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.
7Motero nanunso mudakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse a ku Masedoniya ndi a ku Akaiya.
8Inde kuchokera kwa inu mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu.
9Iwo amakamba okha za m'mene mudatilandirira, ndi za m'mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira.
10Tsopano mukudikira Mwana wake kuti abwerenso kuchokera Kumwamba. Mwana wakeyo ndi Yesu, amene Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ulikudza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.