Mas. 147 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kutamanda Mulungu Wamphamvuzonse

1Tamandani Chauta!

Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu,

nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.

2Chauta akumanga Yerusalemu,

akusonkhanitsa Aisraele omwazika.

3Akuchiritsa a mtima wachisoni,

ndipo akumanga mabala ao.

4Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi,

zonse amazitcha maina ake.

5Mbuye wathu ndi wamkulu,

ndipo ndi wa mphamvu zambiri,

nzeru zake nzopanda malire.

6Amakweza oponderezedwa,

koma amagwetsa pansi anthu oipa.

7Imbirani Chauta mothokoza,

imbirani Mulungu wathu nyimbo yokoma ndi pangwe.

8Amaphimba zakumwamba ndi mitambo,

amapatsa nthaka mvula,

amameretsa udzu pa magomo.

9Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi

pamene akulira chakudya.

10Mphamvu za kavalo saziyesa kanthu,

mphamvu za ankhondo sazisamala.

11Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa,

amene amadalira chikondi chake chosasinthika.

12Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu.

Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.

13Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako.

Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe.

14Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako,

amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala.

15Akapereka lamulo pa dziko lapansi,

mau ake amayenda mwaliŵiro.

16Amagwetsa chisanu chambee ngati ubweya.

Amamwaza chipale ngati phulusa.

17Amagwetsa matalala ngati miyala.

Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?

18Akalamula kuti zichoke,

pomwepo zimasungunuka,

akaombetsa mphepo, madzi amayenda.

19Amadziŵitsa Yakobe mau ake,

amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake.

20Sadachitepo zimenezi

ndi mtundu wina uliwonse wa anthu,

iwo sadziŵa malangizo ake.

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help