1Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha.
2Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idaŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera.
3Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye.
4Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.”
5 adadzafunsa Petro kuti, “Kodi aphunzitsi anuŵa sakhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu?”
25Iye adati, “Amakhoma.” Tsono Petro ataloŵa m'nyumba, asananene chilichonse, Yesu adamufunsa kuti, “Iwe Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu apansipano amalandira msonkho kwa yani? Kwa anthu a mtundu wao, kapena kwa alendo?”
26Petro adati, “Kwa alendo.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Tsono ndiye kutitu anthu a mtundu wao sayenera kukhoma.
27Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.