Mas. 108 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizo polimbana ndi adaniNyimbo. Salmo la Davide.

1Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka,

ndithu, mtima wanga wakonzekadi!

Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda.

Lumpha, iwe mtima wanga.

2Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani.

Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga.

3Ndidzakuthokozani, Inu Chauta,

pakati pa mitundu ya anthu.

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani

pakati pa anthu a m'maiko onse,

4pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu,

chofika mpaka pamwamba pa mlengalenga,

kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.

5Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse.

Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.

6Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja,

mundiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke.

7Mulungu ali ku malo ake oyera, walonjeza kuti,

“Ndidzakugaŵirani dziko la Sekemu mokondwa,

ndidzakulemberani malire m'chigwa cha Sukoti.

8“Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga.

Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera.

Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu.

9“Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine.

Edomu adzakhala poponda nsapato zanga.

Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.”

10Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga?

Ndani adzanditsogolere ku Edomu?

11Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya,

ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu.

12Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo,

pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake.

13Mulungu akakhala nafe,

tidzamenya nkhondo molimba mtima,

pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help