Owe. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo ya Debora ndi Baraki.

1Tsiku limenelo la kupambana kwa Debora ndi Baraki,

mwana wa Abinowamu, adaimba nyimbo iyi yakuti,

2“Pakuti atsogoleri adatsogoleradi m'dziko la Israele,

ndipo anthu adadzipereka okha mwaufulu,

tamandani Chauta.

3“Imvani, inu mafumu,

tcherani khutu, inu olamulira.

Ndidzaimba nyimbo yokoma,

kuimbira Chauta, Mulungu wa Israele.

4“Inu Chauta, pamene munkatuluka m'Seiri,

pamene munkayenda kuchokera ku Edomu,

dziko lidagwedezeka,

kumlengalenga kudanjenjemera,

mitambo idasungunuka nigwetsa madzi.

5 Eks. 19.18 Mapiri adagwedezeka pamaso pa Chauta,

phiri la Sinai lidagwedezeka pamaso pa Chauta,

Mulungu wa Aisraele.

6“Pa nthaŵi ya Samigara, mwana wa Anati,

pa nthaŵi ya Yaele, m'miseu munali zii,

alendo ankangolambalala m'tinjira takumbali.

7Anthu adaathaŵa ku midzi,

midzi idaatha ku Israele,

mpaka pamene iwe Debora udafika,

udafika ngati mai ku Israele.

8Pamene anthu adasankhula milungu ina,

nkhondo idafika m'dziko.

Mwa anthu 40,000 ku Israele,

ndani adatenga chishango kapena mkondo?

9Mtima wanga uli ndi atsogoleri a ankhondo a ku Israele,

uli ndi anthu amene adadzipereka mwaufulu,

kudzipereka mwaufulu pakati pa anzao.

Tamandani Chauta!

10“Inu okwera pa abulu oyera ambee,

inu okwera pa zishalo,

ndi inu oyenda pa mseu,

musimbe zimenezi.

11Ku zitsime oimba akuimba nyimbo

zokondwerera kuti Chauta wagonjetsa,

zokondwerera kuti anthu ake ku Israele apambana.”

“Tsono anthu a Chauta adasonkhana

kuchokera ku midzi yao.

12“Adati,

‘Tsogolera ndiwe Debora, tsogolera,

tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.

Pita patsogolo Baraki, tsogolera akapolo ako,

iwe mwana wa Abinowamu.’ ”

13Pambuyo pake anthu okhulupirika

adabwera kwa atsogoleri ao,

anthu a Chauta adapita kukamenyera Chauta nkhondo,

polimbana ndi adani amphamvu.

14Adakaloŵa m'chigwa kuchokera ku Efuremu,

akukutsata iwe Benjamini, pamodzi ndi achibale ako.

Kwa Makiri kudachokera atsogoleri a ankhondo,

kwa Zebuloni kudachokera onyamula ndodo yaudindo.

15Olamulira a Isakara adabwera ndi Debora,

anthu a kwa Isakara adatsatanso Baraki,

nathamangira ku zigwa akumutsata.

Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo,

osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.

16Chifukwa chiyani ankachedwa ku makola a nkhosa,

kumangomvetsera zitoliro zoitanira nkhosa?

Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo,

osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.

17Agiliyadi adatsala patsidya pa Yordani.

Nawonso anthu a kwa Dani,

chifukwa chiyani ankachedwa m'zombo?

Aasere ankangokhala m'madooko pa gombe la nyanja,

ankangokhala m'madooko mwao.

18Azebuloni ndi fuko

limene lidaika moyo wake m'zoopsa.

Nawonso Anafutali adaika moyo wao pa minga,

pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.

19“Mafumu adabwera namenya nkhondo,

mafumu a ku Kanani adamenya nkhondo

ku Taanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,

koma sadapateko zofunkha zasiliva,

kapena china chilichonse.

20Ngakhale nyenyezi zakumwamba zidamenya nkhondo,

zidathira nkhondo Sisera,

zikuyenda m'njira zake mu mlengalenga.

21Chigumula cha madzi a mtsinje wa Kisoni

chidaŵakokolola onsewo,

madzi othamanga, madzi amphamvu a Kisoni.

Mtima wanga, limbika, yenda mwamphamvu!

22“Tsono ziboda za akavalo zidamveka kwambiri,

akavalo ali paliŵiro,

akuthamanga kwambiri.

23“Mngelo wa Chauta akuti,

‘Utemberere Merozi,

utemberere koopsa nzika zake,

chifukwa chakuti sizidabwere kudzathandiza Chauta,

pakulimbana ndi adani ake amphamvu.’

24“Yaele, mkazi wa Hebere Mkeni,

akhale wodala kupambana akazi onse,

ndithudi akhale wodala kupambana akazi onse am'dziko.

25Munthu uja adapempha madzi akumwa,

koma Yaele adamupatsa mkaka,

adamupatsa chambiko m'chikho chachifumu.

26Adatenga chikhomo cha hema

natenganso nyundo m'dzanja lake lamanja,

adakhoma nacho Sisera, naphwanya mutu wake,

adamutswanya ndi kumuboola m'litsipa mwake.

27Sisera adathifuka naagwa;

adangoti thasa ku mapazi a Yaele.

Adathifukadi nagwera ku mapazi a Yaele.

Kumene adaathifukirako, adagwera komweko, naafa.”

28Mai wake a Sisera adasuzumira pa zenera, nanena kuti,

“Chifukwa chiyani galeta lake silikufika msanga?

Bwanji mdidi wa akavalo a magaleta ake ukuchedwa?

29Amai ake anzeru kopambana adamuyankha,

mwiniwake yemwenso adadziyankha yekha kuti,

30‘Kodi sakufunafuna zofunkha kuti agaŵane?

Akugaŵira wankhondo aliyense mkazi mmodzi kapena aŵiri.

Akugaŵira Sisera zofunkha,

zovala zonyika mu utoto,

zovala zopeta zonyika mu utoto,

zovala ziŵiri zonyika mu utoto,

zopeta kuti ndizivala m'khosi?’

31“Motero Inu Chauta, adani anu aonongeke!

Koma abwenzi anu akhale ngati dzuŵa

lotuluka ndi mphamvu zake zonse.”

Tsono dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help