Yos. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mizinda yopulumukiramo.

1 Num. 35.9-34; Deut. 4.41-43; 19.1-13 Chauta adauza Yoswa kuti,

2“Uza Aisraele kuti, ‘Sankhulani mizinda yopulumukiramo, imene Ine ndidakuuzani kudzera mwa Mose.

3Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi, osati mwadala, angathe kuthaŵira kumeneko. Motero angathe kupulumuka kwa wofuna kumlipsira.

4Angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyo, nakafika pa malo achiweruzo amene ali pa chipata cha mzindawo. Atafika, asimbire atsogoleri mlandu wakewo. Apo atsogoleriwo adzamlola kuloŵa mumzindamo, nadzampatsa malo oti azikhalako.

5Munthu wofuna kulipsirayo akamlondola komweko, anthu amumzindamo asampereke munthu wopha mnzakeyo. Koma amtchinjirize chifukwa adachita zimenezo mwangozi, pakupha Mwisraele mnzake. Sadachite zimenezo mwachiwembu.

6Munthuyo adzakhala mumzindamo mpaka ataweruzidwa pamaso pa anthu onse, ndiponso mpaka mkulu wa ansembe wa nthaŵi imeneyo atafa. Pamenepo munthuyo angathe kubwereranso kwao, kumudzi kumene adachoka mothaŵa kuja.’ ”

7Motero cha kuzambwe kwa mtsinje wa Yordani adapatula Kedesi m'dera la Galilea, m'dziko lamapiri la Nafutali. M'dziko lamapiri la Efuremu adapatula Sekemu, ndipo m'dziko lamapiri la Yuda adapatula Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni).

8Kuvuma kwa Yordani, m'mapiri aja a kuvuma kwa Yeriko m'chipululu muja, adapatula Bezeri pakati pa mizinda ya fuko la Rubeni. Pakati pa mizinda ya fuko la Gadi ku Giliyadi adapatula Ramoti. Ndipo pakati pa mizinda ya fuko la Manase ku Basani adapatula Golani.

9Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraele onse, ngakhalenso alendo amene ankakhala pakati pao. Aliyense wopha munthu mwangozi, osati mwadala, ankatchinjirizidwa kumeneko. Womlondola kuti amlipsire sankaloledwa kumupha munthu wothaŵayo, mlandu wake usanazengedwe pamaso pa mpingo wonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help