1Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.
2Anali kwa Mulungu chikhalire.
3Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.
4Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu.
5Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako.
6 tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.”
22Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikaŵafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?”
23Yes. 40.3Yohane adaŵayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya:
“Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu;
akunena kuti,
‘Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.’ ”
24Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi.
25Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?”
26Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa.
27Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake.”
28Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza.
Yesu ndiye Mwanawankhosa wa Mulungu29M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
30Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.’
31Inenso sindinkamudziŵa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziŵe.”
32Yohane adachitanso umboni, adati, “Ndidaona Mzimu Woyera akutsika kumwamba ngati nkhunda, nakhazikika pa Iye.
33Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’
34Ineyo ndidaziwonadi, ndipo ndikuchita umboni kuti ameneyu ndi Mwanadi wa Mulungu.”
Ophunzira oyamba a Yesu35M'maŵa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena aŵiri.
36Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.”
37Ophunzira aŵiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu.
38Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi ulendowu?” Iwo adati, “Timati tidziŵe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.)
39Yesu adati, “Tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthaŵi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo.
40Mmodzi mwa aŵiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, mbale wake wa Simoni Petro.
41Iye adayamba kukapeza mbale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.)
42Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)
Yesu aitana Filipo ndi Natanaele43M'maŵa mwake Yesu adaganiza zopita ku Galileya. Adapeza Filipo, namuuza kuti, “Unditsate.”
44Filipo anali wa ku mudzi wa Betsaida, kwaonso kwa Andrea ndi Petro.
45Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.”
46Koma Natanaele adamufunsa kuti, “Kodi ku Nazarete nkuchokera kanthu kabwino?” Filipo adati, “Tiye ukadziwonere wekha.”
47Pamene Yesu adaona Natanaele akubwera potero, adati, “Mwamuwonatu Mwisraele weniweni wopanda chinyengo.”
48Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.”
49Natanaele adati, “Aphunzitsi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israele.”
50Yesu adamuyankha kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuwona patsinde pa mkuyu paja? Udzaona zoposa pamenepa.”
51Gen. 28.12Adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti mudzaona Kumwamba kutatsekuka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.