1“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraele,
bwererani kwa Ine,”
akuterotu Chauta.
“Chotsani mafano anu amene akundinyansaŵa,
ndipo musasokerenso.
2Muzilumbira moona kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’
Muzichita zimenezi mwachilungamo ndi mokhulupirika.
Mukatero, anthu a mitundu yonse adzandipempha
kuti ndiŵadalitse, ndipo adzanditamanda.”
3 Hos. 10.12 Chauta akuuza anthu a ku Yuda ndi anthu
okhala ku Yerusalemu kuti, “Limani masala anu,
musabzale pakati pa minga.
4Muzikhala okhulupirika
ndi kumanditumikira Ine Chauta ndi mtima wanu wonse.
Muzichita zimenezi inu anthu a ku Yuda
ndi inu okhala ku Yerusalemu,
kuwopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto,
ndi kukuyakirani chifukwa cha ntchito zanu zoipa,
osapezeka wina aliyense wotha kuuzimitsa.”
Adani ochokera kumpoto kwa Yuda5Lalika ku Yuda, lengeza ku Yerusalemu kuti,
“Lizani lipenga m'dziko lonse,
ndi kufuula kuti,
‘Sonkhanani,
tiyeni tipite ku mizinda ku Ziyoni.’
6Kwezani mbendera ku Ziyoni.
Musachedwe, thaŵani kuti mupulumuke.
Chauta akubweretsa chilango kuchokera kumpoto,
kudzakhala chiwonongeko chachikulu.
7Monga momwe mkango umatulukira m'ngaka yake,
momwemonso woononga maiko wanyamuka.
Watuluka m'malo mwake kuti asakaze dziko lanu.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda okhalamo.
8Motero valani ziguduli,
mudandaule ndi kulira kwambiri.
Pakuti mkwiyo woopsa wa Chauta sudatichoke.”
9Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo mfumu ndi nduna zake, onse adzataya mtima. Ansembe adzaopsedwa, ndipo aneneri adzangoti kakasi.”
10Tsono ndidati, “Ha, Ambuye Chauta, ndithu mudaŵanyenga anthu aŵa pamodzi ndi a mu Yerusalemu! Mudaŵauza kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ koma chonsecho lupanga lili pamutu pao.”
11Nthaŵiyo ikadzafika, anthu a mu Yerusalemu adzaŵauza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo am'chipululu ikukuntha pa anthu anga, osatitu mphepo yopetera kapena kuyeretsera zinthu ai.
12Imeneyo ndi mphepo yamphamvu zedi yochokera kwa Ine Mulungu. Ndipo ndi Ineyo amene ndikuŵaimba mlandu.”
13Onani, adani akubwera mwaliŵiro ngati mitambo,
magaleta ao akuthamanga ngati kamvulumvulu.
Akavalo ao ngaliŵiro kuposa chiwombankhanga.
Kalanga ine, taonongeka.
14Iwe Yerusalemu,
chotsa zoipa mumtima mwako kuti upulumuke.
Kodi maganizo ako oipa udzakhala nawobe mpaka liti?
15Pakuti amithenga a ku Dani akulalika mau,
akulengeza zoopsa kuchokera ku Phiri la Efuremu.
16Akuti, “Muchenjeze mitundu ya anthu
kuti mdani akubwera.
Mulengeze kwa anthu a mu Yerusalemu
kuti ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,
akufuula ndi kudzathira nkhondo mizinda ya Yuda.
17Akuzinga Yerusalemu ngati alonda a munda,
chifukwa choti anthu andipandukira,”
akuterotu Chauta.
18“Zimenezi zakugwerani, inu Ayuda,
chifukwa cha makhalidwe anu oipa ndi zochita zanu.
Chimenechi ndiye chilango chanu,
nchoŵaŵa kwambiri,
chokalasa mpaka ku mtima.”
Yeremiya amvera chisoni anthu ake19Mayo, mayo, ati kupweteka ati!
Ha, mtima wanga ukuŵaŵa,
ukugunda moti thithithi.
Sindingathe kukhala chete.
Ndikumva kulira kwa lipenga ndi mfuu yankhondo.
20Tsoka limatsata tsoka linzake,
ndipo dziko lonse lasanduka bwinja.
Mwadzidzidzi mahema athu aonongeka,
machinga ake agwetsedwa pa kanthaŵi kang'onong'ono.
21Kodi ndikhale ndikuwona mbendera yankhondo mpaka liti?
Kodi ndikhale ndikumva lipenga mpaka liti?
22Chauta akuti “Paja anthu anga ndi opusa,
Ine sandidziŵa.
Ali ngati ana opulukira,
osamvetsa chilichonse.
Ali ndi luso pochita zoipa,
koma kuchita zabwino sadziŵa.”
Yeremiya aona kubwera kwa chiwonongeko m'masomphenya23Ndidayang'ana dziko lapansi,
linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu kalikonse.
Ndidayang'ana thambo,
linalibe konse kuŵala.
24Ndidayang'ana mapiri, ankagwedezeka,
ndipo magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25Ndidayang'ana, osaona ndi munthu mmodzi yemwe,
ndipo mbalame zonse zamumlengalenga zinali zitathaŵa.
26Ndidayang'ana, dziko la chonde linali
litasanduka chipululu,
mizinda yake yonse inali itasanduka mabwinja,
chifukwa cha mkwiyo wa Chauta.
27Chauta akunena kuti,
“Dziko lonse lidzasanduka chipululu,
komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28Chifukwa cha zimenezi dziko lonse lapansi
lidzalira ndipo zakumwamba zidzachita mdima.
Pakuti Ine ndalankhula, ndipo ndili ndi cholinga.
Sindidafeŵe mtima, ndipo sindidzabwerera konse m'mbuyo.”
29Anthu a m'mudzi uliwonse adzathaŵa,
pakumva phokoso la ankhondo okwera pa akavalo
ndi oponya mivi.
Azikati uku ena akuloŵa m'nkhalango,
ena akukwera m'mathanthwe.
Mizinda yonse kuisiya,
popanda ndi mmodzi yemwe wokhalamo.
30Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja.
Ukuti utani m'mene ukuvala zofiira,
m'mene ukuvala zokongoletsa zagolide,
m'mene ukukuza maso ako poŵapaka zokometsera?
Ukungodzivuta poyesa kudzikongoletsa.
Zibwenzi zako zikukunyoza,
zikufuna kulanda moyo wako.
31Ndidamva kulira ngati kwa mkazi
pa nthaŵi yake yochira,
kubuula ngati kwa mkazi pa uchembere wake woyamba.
Kumeneku kunali kulira kwa anthu a mu Ziyoni,
ŵefuŵefu,
atatambalitsa manja ao, akunena kuti,
“Tsoka ife! Tikukomoka,
moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.