Bar. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Nchifukwa chake Ambuye Mulungu wathu achitadi zimene adaaneneratu, zakuti adzatilanga ifeyo ndi aweruzi athu a ku Israele, ndi mafumu athu ndi akalonga athu, ndiponso anthu a ku Israele ndi a ku Yuda.

2Zimene Iye adazichita ku Yerusalemu monga zidalembedwera m'malamulo a Mose, zinthu zotere sizidachitikepo pansi pano.

3Zinali zakuti tizizunzika mpaka kudya mnofu wa ana athu, wina mwana wake wamwamuna, wina mwana wake wamkazi.

4Ambuye adaŵasandutsa akapolo a mafumu onse otizungulira. Dziko lathu adalisandutsa chipululu, ndipo dzina lathu lidasanduka lonyozeka pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene adatibalalitsa.

5Choncho tidasanduka akapolo m'malo mokhala aufulu, chifukwa tidaachimwira Ambuye Mulungu wathu pakusamvera mau ao.

6“Ambuye Mulungu wathu ngolungama, koma tsopano manyazi atigwira ifeyo pamodzi ndi makolo athu.

7Zoopsa zonse zimene Ambuye adatichenjeza, zatigweradi lero.

8Komabe sitidapemphe konse kukoma mtima kwa Ambuye pakusiya maganizo oipa a m'mitima mwathu.

9Nchifukwa chake Ambuye adatisungira zoopsazo nazigwetsa pa ife, popeza kuti Iwo ngolungama pa ntchito zonse zimene adatilamula.

10Komabe ife sitidamvere mau ao kapena kutsata malamulo amene adatipatsa.

Pemphero lopempha chipulumutso

11“Inu Ambuye, Mulungu wa Israele, mudatulutsa anthu anu ku dziko la Ejipito ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi zozizwitsa ndiponso zodabwitsa, ndi mphamvu yaikulu ndiponso dzanja lotambalitsa, ndipo mudamveketsa dzina lanu mpaka lero lino.

12Koma ife tidachimwa, tidachita zoipa ndi zosalungama posatsata konse malamulo anu, Inu Ambuye Mulungu wathu.

13Mutichotsere mkwiyo wanu, popeza kuti tangotsala oŵerengeka pakati pa mitundu ya anthu kumene mudatibalalitsa.

14Ambuye, imvani pemphero lathu ndi kupemba kwathu. Mutipulumutse kuti dzina lanu lisanyozedwe, ndipo mutikomere mtima pamaso pa onse amene adatitenga kupita nafe ku ukapolo,

15Choncho anthu onse a pa dziko lapansi adzadziŵa kuti Inu ndinu Ambuye Mulungu wathu, popeza kuti Aisraele ndi zidzukulu zao amatchulidwa dzina lanu.

16“Inu Ambuye, yang'anani pansi kuchokera ku nyumba yanu yoyera, ndipo mutikumbukire. Tcherani khutu Ambuye ndipo mumvetsere.

17Phenyulani maso Ambuye ndipo muwone. Akufa amene ali m'manda, amene mpweya udachotsedwa m'thupi mwao, sangathe kukubwezerani ulemu kapena kuyamikira chilungamo chanu.

18Koma munthu wamoyo, amene akumva chisoni mumtima mwake, amene akuyenda choŵerama ali wolefuka, amene maso ake sakupenyanso bwino ndipo akumva njala, ameneyo ndiye amene angathe kukubwezerani ulemu ndi kuyamikira chilungamo chanu, Inu Ambuye.

19“Ambuye Mulungu wathu, tikupempha chifundo chanu, koma osati chifukwa cha ntchito zolungama za makolo athu ndi za mafumu athu.

20Inu mudatiwonetsa mkwiyo wanu ndi ukali wanu, monga momwe mudaatichenjezera kudzera mwa atumiki anu, aneneri aja. Iwo ankatiwuza kuti,

21Yer. 7.34; 27.10-12‘Ambuye akuti, Ŵeramitsani mapewa anu, gonjerani mfumu ya ku Babiloni ndi kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndidaapatsa makolo anu.

22Koma mukapanda kumvera Ambuye ndi kutumikira mfumu ya ku Babiloniyo,

23ndidzathetsa mfuu wachimwemwe ndi wachisangalalo wa mkwati wamkazi ndi wamwamuna ku mizinda ya ku Yuda ndiponso ku dera lozungulira Yerusalemu. Motero dziko lonse lidzasanduka chipululu, mosakhalanso anthu.’

24 Yer. 8.1, 2 “Koma ife sitidamvere mau anu kapena kutumikira mfumu ya ku Babiloni. Tsono mudachitadi zimene mudatichenjeza kudzera mwa atumiki anu aneneri, zakuti mafupa a mafumu athu ndi a makolo athu adzaŵatulutsa m'manda mwao.

25Adaŵaikadi pa dzuŵa masana, ndipo pa chisanu usiku. Iwowo adafa imfa yoopsa ndi njala, lupanga ndiponso mliri.

26Tsono Nyumba imene inkatchulidwa dzina lanu, yasanduka monga m'mene ikuwonekeramu, chifukwa cha zolakwa za fuko la Israele ndi la Yuda.

27“Komabe Inu Ambuye Mulungu wathu, mudatimvera chisoni ndi kutichitira chifundo.

28Deut. 28.58, 62Mudachita monga momwe mudalengezera kudzera mwa Mose, mtumiki wanu, tsiku limene mudamlamula kulemba Malamulo anu pamaso pa ana a Israele. Paja mudanena kuti,

29‘Mukapanda kumvera mau anga, gulu lalikulu la anthuli ndidzalichepetsa kwabasi pakati pa mitundu ya anthu kumene ndidzaŵabalalitsa.

30Ndikudziŵa kuti anthu ameneŵa sadzandimvera, chifukwa ngokanika. Koma kudziko kumene adzapite nawo atatengedwa ukapolo, adzadzidzimuka.

31Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu wao. Tsono ndidzaŵapatsa mtima womvetsa zinthu ndi makutu omvera zinthu.

32Motero adzanditamanda kudziko kumene adzapite nawo atatengedwa ukapolo, ndipo adzakumbukira dzina langa.

33Kukanika kwao kudzatha, adzasiya ntchito zao zoipa, chifukwa azidzakumbukira zimene zidagwera makolo ao pamene adachimwira Ambuye.

34Choncho ndidzaŵabwezeranso ku dziko limene ndidaalonjeza kuti ndidzapatsa makolo ao Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndipo azidzalilamulira. Ndidzaŵachulukitsa, sadzakhalanso ochepa.

35Yer. 32.38-40Ndidzapangana nawo chipangano chosatha, chakuti Ine ndidzakhala Mulungu wao ndipo iwo adzakhala anthu anga. Sindidzaŵachotsanso anthu anga Aisraele ku dziko limene ndidaŵapatsa.’

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help