1Tamandani Chauta!
Mtamandeni, inu atumiki ake,
tamandani dzina la Chauta.
2Yamikani Chauta
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3Dzina la Chauta litamandike
kuyambira ku matulukiro a dzuŵa
mpaka ku maloŵero ake.
4Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse,
ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga.
5Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu,
amene akukhala kumwamba,
6wochita kuŵeramira pansi
poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi.
7Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi,
ndipo amatulutsa ku dzala anthu osoŵa.
8Amaŵakhazika pamodzi ndi mafumu,
mafumu a anthu a Chauta.
9Amapatsa banja mkazi wosabala,
namsandutsa mai wosangalala wa ana.
Tamandani Chauta!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.