Hab. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndidzakhala ngati mlonda,

woimirira pa linga.

Ndidzaona zimene adzandiwuze,

apo ndidzadziŵa zimene adzayankhe za dandaulo langa.

Yankho la Chauta

2Chauta adandiyankha kuti,

“Lemba uthengawu,

ulembe mooneka bwino pa mapale,

kuti woŵerenga aŵerenge mosavuta.

3 kwake.

5Monga munthu wokhuta vinyo ali wosokonezeka,

chonchonso munthu wodzitama ndi wosakhazikika.

Ndi waumbombo kwambiri ngati manda,

ngati imfa amakhala wosakhuta.

Amagwira anthu a mitundu yonse,

amaŵasonkhanitsa ngati ake.”

6Koma ogwidwawo adzamnyoza,

adzamnyodola ponena kuti,

“Tsoka kwa amene amadzikundikira chuma

chosakhala chake,

amene amalemera ndi ngongole zosalungama.

Adzatero mpaka liti?”

7Angongolewo adzakuukira mwadzidzidzi.

Adzakuchititsa mantha ndi kukulanda zako zonse.

8Chifukwa iweyo udafunkha mitundu yambiri ya anthu,

koma otsala adzakufunkha iweyo,

chifukwa chokhetsa magazi a anthu ambiri,

ndiponso chifukwa choononga mwankhanza

mizinda ndi onse okhalamo.

9Tsoka kwa amene amalemera ndi phindu

lobera anzake, kuti akweze malo ake

ndi kupewa zovuta.

10Udafuna kuwononga anthu a mitundu yambiri

koma potero wachititsa manyazi banja lako,

ndipo wataya moyo wako.

11Ndi njerwa zomwe za nyumba yako

zidzafuula chidzudzulo,

ndipo mitanda idzathira mang'ombe ake.

12Tsoka kwa amene wamanga mzinda pokhetsa magazi,

ndipo waukhazikitsa pozunza anthu.

13 Mphu. 14.19 Koma Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza

kuti zimene anthu amagwirira ntchito zili

ngati nkhuni pa moto.

Anthu a mitundu yonse amangodzitopetsa popanda phindu.

14 Yes. 11.9 Motero anthu onse adzazindikira ulemerero

wa Chauta kuti ndi wodzaza,

monga momwe madzi amadzazira nyanja.

15Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zaukali,

amene amaŵaledzeretsa kuti aŵachititse manyazi.

16Koma amene udzachite manyazi ndiwe

ndipo onse adzakunyoza kwambiri.

Tsopano imwa ndiwe, mpaka kudzandira.

Chikho cha chilango cha Chauta chikupeza,

ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.

17Udzachita mantha chifukwa cha kusakaza

nkhalango za ku Lebanoni.

Udzaopsedwa chifukwa cha kuwononga nyama zake.

Wakhetsa magazi a anthu mwankhanza,

waononga mizinda ndi onse okhalamo.

18Kodi phindu la fano nchiyani?

Adalipanga ndi munthu.

Ndi chifanizo chabe, ndipo nchinthu chonyenga.

Munthu wopangayo amakhulupirira zimene wachita,

koma mafano akewo satha nkulankhula komwe.

19Tsoka kwa amene amauza mtengo kuti, “Nyamuka!”

Amene amauza mwala waduu kuti, “Dzuka!”

Kodi zimenezi zingathe kulangiza?

Nzopangidwa ndi golide ndi siliva,

ndipo sizitha konse kupuma.

20Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera.

Dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help