Mas. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yotamanda Chauta.

1Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake.

Zoonadi ochita zolungama azitamanda.

2Tamandani Chauta ndi pangwe.

Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.

3Muimbireni nyimbo yatsopano,

kodolani nsambozo mwaluso ndi kufuula

mosangalala.

4Mau a Chauta ndi olungama,

zochita zake zonse amazichita mokhulupirika.

5Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera.

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

6Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa.

Zonse zakumeneko zidalengedwa

pamene Iye adalankhula mau ake.

7Adasonkhanitsa pamodzi madzi a m'nyanja zakuya

ndipo adaziikira malire kuti zisasefukire.

8Dziko lonse lapansi liwope Chauta.

Anthu onse okhala pa dziko lapansi achite naye mantha,

9pakuti Iye adalankhula, ndipo zidachitikadi,

adalamula, ndipo zidaonekadi.

10Zolinga za anthu akunja

Chauta amazisandutsa zopandapake.

Maganizo ao onse amaŵasandutsa achabechabe.

11Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse,

maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.

12Ngwodala mtundu wa anthu

amene Mulungu wao ndi Chauta,

anthu amene Chauta waŵasankha akeake.

13Chauta ali kumwamba,

amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse.

14Kumene amakhala pa mpando wachifumuko,

amapenya anthu onse okhala pa dziko lapansi

15Amene amapanga mitima ya anthu onse,

ndiye amene amapenya ntchito zao zonse.

16 Yud. 9.7; 1Am. 3.19 Mfumu siipulumuka

chifukwa cha kukula kwa gulu lake la ankhondo.

Wankhondo sapulumuka

chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri.

17Pa kavalo wankhondo sungaikepo mtima kuti upambane,

chifukwa sangathe kupulumutsa munthu,

ngakhale kavaloyo ali ndi mphamvu zambiri.

18Chauta amayang'ana anthu omumvera,

ndi odalira chikondi chake chosasinthika.

19Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa

ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.

20Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.

21Mitima yathu imasangalala mwa Chauta,

popeza kuti timadalira dzina lake loyera.

22Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika

chikhale pa ife,

chifukwa timakhulupirira Inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help