1Chaka chachitatu cha ufumu wa Belisazara, ine Daniele ndidaona zinthu kachiŵiri m'masomphenya.
2Ndidaona kuti ndinali mu mzinda waukulu wa Susa umene uli m'chigawo cha Elamu. Ndidaonanso kuti ndinali ku mtsinje wa Ulai.
3Tsono nditatukula maso, ndidaona nkhosa yamphongo ya nyanga ziŵiri, itaima pa gombe la mtsinjewo. Nyanga ziŵirizo zinali zitalizitali, koma imodzi inali yaitali kupambana inzake, ndipo idaamera inzakeyo itamera kale.
4Ndidaona nkhosa yamphongoyo ikuthamanga chakuzambwe, chakumpoto ndi chakumwera. Panalibe chilombo china chotha kulimbana nayo, ndipo panalibe wotha kulanditsa kanthu kwa iyo. Choncho inkachita zimene inkafuna, nimaonetsa mphamvu zake monyada.
5Ndikulingalira zimenezi, ndidaona tonde akuchokera kuzambwe, kumadutsa dziko lonse lapansi, akuyenda m'malere mokhamokha. Anali ndi nyanga yaikulu pakati pa maso ake.
6Adayandikira nkhosa yamphongo ya nyanga ziŵiri ija, imene ndidaona itaima pa gombe la mtsinje, ndipo adaithamangira mwaukali.
7Ndidaona akulimbana ndi nkhosayo mwaukali, naigunda ndi kuthyola nyanga zake ziŵiri zija. Nkhosa ija sidalimbike, tondeyo adaigwetsa pansi namaipondereza. Panalibe woti nkupulumutsa nkhosa yamphongoyo.
8Tsono tonde uja adayamba kudzikuza kwambiri chifukwa cha mphamvu zake. Koma pamene mphamvu zake zidadzafika pokula kwambiri, nyanga yake yaikulu ija idathyoka, pamalo pakepo nkuphuka nyanga zina zinai zazikulu zoloza ku mphepo zonse zinai.
9Pa imodzi mwa nyanga zinaizo padaphuka kanyanga kakang'ono, kamene kadakula kwambiri kuloza kumwera ndi kuvuma ndiponso ku dziko lokondweretsa lija.
10Nyangayo idakula kwambiri mpaka kukafika ku magulu ankhondo akumwamba. Idagwetsa magulu ena a nyenyezi ndi kuzipondereza.
11Idayamba kudzikuza ndithu kwambiri mpaka kufuna kulimbana ndi mfumu ya magulu akumwamba. Idathetsa nsembe zimene zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku, ndipo idagwetsa nyumba yopembedzeramo mfumuyo.
12Magulu akumwamba aja adagonja kwa iyo, nsembe za tsiku ndi tsiku zoperekera machimo idazithetsa ndipo idagwetseratunso chipembedzo choona. Ai, nyangayo idapambanadi pa zonse zimene inkachita.
13Tsono ndidamva woyera wina akulankhula. Woyera winanso adafunsa amene ankalankhulayo kuti, “Kodi zidzatha liti zinthu zimene zikuwoneka m'masomphenyazi? Kodi nsembe za tsiku ndi tsiku zidzaletsedwa mpaka liti? Nanga Chonyansa chosakazachi chidzakhalapo mpaka liti? Kodi malo oyera pamodzi ndi magulu ankhondo akumwambawo adzaleka liti kumaponderezedwa?”
14Winayo adayankha kuti, “Zidzachitika mpaka patapita madzulo ndi m'maŵa a masiku 2,300. Pambuyo pake malo oyerawo adzaŵakwezanso monga kale.”
Mngelo Gabriele amasulira zooneka m'masomphenyazo15Ine Daniele ndinkati ndikaona zinthu m'masomphenya, ndinkayesetsa kuti ndizimvetsa. Mwadzidzidzi ndidaona wina wa maonekedwe a munthu, ataima kutsogolo kwanga.
16Kenaka ndidamva liwu la munthu kuchokera pakati pa magombe a mtsinje wa Ulai. Liwulo lidati, “Iwe Gabriele, mmasulire munthuyo zimene adaziwona m'masomphenyazo.”
17Motero Gabrieleyo adabwera kumene ine ndidaaima. Atafika, ndidagwidwa ndi mantha, ndipo ndidadzigwetsa chafufumimba. Koma iye adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, umvetse kuti zimene udaziwona m'masomphenyazo zikunena za nthaŵi yomaliza.”
18Akulankhula choncho, ine ndidadzigwetsa pansi chafufumimba, nthaŵi yomweyo ndafa nato tulo! Koma iye adandikhudza nandikhazikanso chachilili.
19Tsono adandiŵuza kuti, “Ndikudziŵitsa zimene zidzachitike ukadzatha mkwiyo, pakuti zimenezi ndi za nthaŵi yomaliza.
20Nkhosa yamphongo ya nyanga ziŵiri imene udaiwona ija, ikutanthauza mfumu ya Amedi ndi mfumu ya Apersi.
21Tonde uja ndi mfumu ya Agriki, ndipo nyanga yaikulu ya pakati pa maso ija ndiye mfumu yoyamba.
22Kunena za nyanga yothyoka ija, imene pamaso pake padaphuka nyanga zinai, ndiye kuti m'dziko lakelo mudzatuluka maufumu anai, koma mphamvu zao sizidzalingana ndi za ufumu woyamba uja.
23“Pa masiku otsiriza a maufumu amenewo, machimo ao atachuluka mpaka kusefukira, padzaoneka mfumu yokhakhala mtima, yochenjera kwambiri.
24Mphamvu zake zidzakhala zazikulu, ndipo adzaononga koopsa. Adzapambana pa zonse zimene adzachita. Adzaononga anthu amphamvu ndiponso anthu oyera mtima.
25Chifukwa cha kuchenjera kwake kwambiri adzakhoza pochita zonyenga, ndipo mtima wake udzadzikuza. Adzaononga anthu ambiri popanda kuŵachenjezeratu. Adzaukira ngakhale mfumu ya mafumu onse. Komabe adzaonongeka, tsonotu osati ndi mphamvu za munthu ai.
26Zimene udaziwona zokhudza madzulo ndi m'maŵa zija nzoona. Koma usunge zimenezi mwachinsinsi, poti mpakale pamene zidzachitike.”
27Tsono kunena za ine Daniele, mphamvu zidaandithera, ndipo ndidaadwala masiku angapo. Kenaka ndidadzuka nkupita kukagwira ntchito kwa mfumu. Koma zimene ndidaaziwona zija zinkandidetsa nkhaŵa, ndipo sindidathe kuzimvetsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.