1 Aef. 6.9 Inu ambuye, antchito anu muzikhalitsana nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziŵa kuti inunso muli ndi Mbuye wanu Kumwamba.
Malangizo ena2Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
3Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.
4Mundipempherere tsono kuti ndichifotokoze bwino monga ndiyenera.
5 Aef. 5.16 Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe.
6Lun. 8.12Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Mau otsiriza7 Ntc. 20.4; 2Tim. 4.12 Aef. 6.21, 22 Tikiko, mbale wathu wokondedwa, adzakudziŵitsani zonse za ine. Iyeyo ndi mtumiki wokhulupirika, wantchito mnzathu pa ntchito ya Ambuye.
8Nchifukwa chake ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti adzakulimbitseni mtima.
9Fil. 1.10-12Ndikumtuma pamodzi ndi Onesimo, mbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali mmodzi mwa inu. Iwo adzakudziŵitsani zonse zakuno.
10 Ntc. 19.29; 27.2; Fil. 1.24; Ntc. 12.12, 25; 13.13; 15.37-39 Aristariko, mkaidi mnzanga, akukupatsani moni. Akuteronso Marko, msuweni wa Barnabasi. Za Markoyo mudalandira kale mau akuti akafika kwanuko, mumlandire bwino.
11Akutinso moni Yesu, wotchedwa Yusto. Mwa ochokera ku Chiyuda ndi atatu okhaŵa amene akundithandiza pa ntchito ya Ufumu wa Mulungu, ndipo andilimbikitsa kwambiri.
12 Akol. 1.7; Fil. 1.23 Akukupatsani moni Epafra, amene ali mmodzi mwa inu, ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu. Nthaŵi zonse iyeyo amalimbikira kukukumbukirani m'mapemphero ake. Amatero pofuna kuti inuyo mukhale okhazikika, angwiro, ndipo kuti muzichilimikira kuchita zonse zimene Mulungu afuna.
13Ndingathe kumchitira umboni kuti amagwira ntchito kwambiri chifukwa cha inu, ndiponso chifukwa cha anthu okhala ku Laodikea ndi ku Hierapoli.
142Tim. 4.11; Fil. 1.24; 2Tim. 4.10; Fil. 1.24Luka, sing'anga wathu wokondedwa, ndiponso Dema, onsewo akuti moni.
15Mutiperekereko moni kwa abale athu okhala ku Laodikea, ndiponso kwa Nimfa ndi kwa ampingo amene amasonkhana kunyumba kwake.
16Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani.
17Fil. 1.2Uzani Arkipo kuti, “Samala bwino kuti ntchito imene Ambuye adakupatsa uziigwira moikapo mtima.”
18Ndi dzanja langalanga ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine Paulo.” Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo. Mulungu akukomereni mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.