Mas. 106 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ubwino wa Chauta pa anthu ake

1 1Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Tamandani Chauta.

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

pakuti chikondi chake nchamuyaya.

2Ndani angathe kufotokoza

za ntchito zamphamvu za Chauta,

ndani angathe kumtamanda kokwanira?

3Ngodala anthu otsata malamulo a Chauta,

anthu ochita zolungama nthaŵi zonse.

4Chauta, mundikumbukire

pamene mukukomera mtima anthu anu.

Mundithandize pamene mukuŵapulumutsa,

5kuti ndiwone zokoma za osankhidwa anu,

kuti ndigaŵane nawo chisangalalo cha mtundu wanu,

kuti ndipeze ulemerero pamodzi ndi anthu anu.

6Ife tachimwa monga makolo athu,

tachita zoipa, sitidachite zabwino.

7 Eks. 14.10-12 Pamene makolo athu anali ku Ejipito,

sadasamale ntchito zanu zodabwitsa.

Sadakumbukire kukula kwa chikondi chanu chosasinthika,

koma adaukira Mulungu Wopambanazonse

ku Nyanja Yofiira kuja.

8Komabe Iye adaŵapulumutsa

malinga ndi ulemerero wa dzina lake,

kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.

9 Eks. 14.21-31 Adalamula Nyanja Yofiira, ndipo idauma,

adaŵatsogolera m'Nyanja yakuya,

iwo nkuyenda pouma.

10Motero adaŵapulumutsa kwa amaliwongo,

naŵalanditsa ku mphamvu za adani ao.

11Ndipo madzi adamiza adani ao onse,

sadatsalepo ndi mmodzi yemwe.

12 Eks. 15.1-21 Tsono anthu ake adakhulupirira mau ake,

naimba nyimbo zomtamanda.

13Koma posachedwa iwo adaiŵala ntchito zake,

ndipo sadayembekeze malangizo ake.

14 Num. 11.4-34 Adadzilekerera

potsata zilakolako zao m'chipululu muja,

adayesa Mulungu m'chipululumo.

15Iye adaŵapatsa zimene iwo adapempha,

koma adatumiza nthenda yoopsa pakati pao.

16 Num. 16.1-35 Nthaŵi ina anthuwo adaachitira kaduka Mose

ndi Aroni, mtumiki wopatulika wa Chauta.

17Pamenepo nthaka idang'ambika nkumeza Datani,

ndipo idakwirira gulu la Abiramu.

18Moto nawonso udabuka m'gulu mwao,

malaŵi a moto adapsereza anthu oipawo.

19 Eks. 32.1-14 Iwo adapanga mwanawang'ombe ku Horebu,

napembedza chifano chosungunula.

20Adasinthanitsa ulemerero wa Mulungu

ndi chifano cha ng'ombe imene imadya udzu.

21Adaiŵala Mulungu Mpulumutsi wao

amene adachita zinthu zazikulu ku Ejipito,

22ntchito zodabwitsa m'dziko la Hamulo,

ndiponso zinthu zoopsa ku Nyanja Yofiira kuja.

23Nchifukwa chake adaŵauza kuti akadaŵaononga,

pakadapanda Mose wosankhidwa wake kuima pamaso pake,

ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usaŵaononge.

24 Num. 14.1-35 Motero iwo adanyoza dziko lokoma,

chifukwa sadakhulupirire malonjezo ake.

25Adang'ung'udza m'mahema mwao

ndipo sadamvere mau a Chauta.

26Nchifukwa chake Iye adakweza dzanja lake

nalumbira kuti anthuwo adzafera m'chipululu,

27 Lev. 26.33 ndipo kuti adzamwaza zidzukulu zao

pakati pa mitundu ina,

ndi kuzibalalitsa m'maikom'maiko.

28 Num. 25.1-13 Anthuwo adayamba kupembedzanso Baala wa ku Peori,

ndi kumadya nawo nsembe zoperekedwa kwa anthu akufa.

29Motero adaputa mkwiyo wa Chauta ndi zochita zaozo,

ndipo mliri udabuka pakati pao.

30Tsono Finehasi, atalanga olakwa,

mliri uja udaleka.

31Motero iyeyo adaŵerengedwa kuti ndi wolungama

ku mibadwo yonse mpaka muyaya.

32 Num. 20.2-13 Anthuwo adakwiyitsa Chauta ku madzi a Meriba kuja,

ndipo zinthu sizidamuyendere bwino Mose

chifukwa cha anthuwo.

33Iwo adampsetsa mtima kwambiri,

kotero kuti Moseyo adalankhula mosalingalira.

34 Owe. 2.1-3; 3.5, 6 Iwo sadaonongeretu mitundu ina ya anthu

monga m'mene Chauta adaaŵalamulira,

35koma adasakanizana ndi mitundu inayo

naphunzira kuchita zoipa zomwe anthu enawo ankachita.

36Adatumikira mafano ao

amene adasanduka msampha kwa iwo.

37 2Maf. 17.17 Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi

kwa mizimu yoipa.

38 Num. 35.33 Adakhetsa magazi osachimwa,

magazi a ana ao aamuna ndi aakazi,

amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani,

choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

39Adadzidetsa ndi ntchito zao,

nakhala osakhulupirika pa zochita zao

ngati mkazi wachigololo.

40 Owe. 2.14-18 Tsono mkwiyo wa Chauta udayakira anthu ake,

chifukwa adanyansidwa nawo anthu akewo.

41Adaŵapereka kwa mitundu ina ya anthu,

kotero kuti amene ankadana nawo,

ndiwo amene ankaŵalamulira.

42Adani ao ankaŵazunza,

ataŵagonjetsa adaŵaika mu ulamuliro wao.

43Nthaŵi zambiri Iye ankaŵapulumutsa,

koma iwo ankamuukirabe osaleka,

namamira m'machimo ao,

44Komabe Chauta adaŵathandiza pa mavuto ao

pamene adamva kulira kwao.

45Adakumbukira chipangano chake

chifukwa cha kuŵakonda anthuwo,

naleza mtima

chifukwa cha kukula kwa chikondi chake chosasinthika.

46Chauta adafeŵetsa mitima ya adani onse

amene adagwira anthu ake ukapolo,

kuti aŵachitire chifundo anthu akewo.

47 1Mbi. 16.35, 36 Tipulumutseni Inu Chauta, Mulungu wathu,

mutisonkhanitse kuchokera pakati pa anthu akunja,

kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera,

kuti tizinyadira pokutamandani.

48Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele,

kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Anthu onse anene kuti, “Inde momwemo.”

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help