Mas. 99 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Eks. 25.22 Chauta ndiye mfumu,

mitundu ya anthu injenjemere.

Wakhala pa akerubi ngati pa mpando wake wachifumu.

Dziko lapansi ligwedezeke!

2Chauta ndi wamkulu ku Ziyoni.

Ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3Onse atamande dzina lake lalikulu ndi loopsa!

Iye ndi woyera!

4Ndinu Mfumu yamphamvu, yokonda chilungamo,

mwakhazikitsa khalidwe losakondera

ndiponso kuweruza kolungama m'dziko la Yakobe.

5Tamandani Chauta, Mulungu wathu,

mpembedzeni ku mpando wake waufumu.

Iye ndi woyera!

6Mose ndi aroni anali ena mwa ansembe ake,

Samuele nayenso anali mmodzi

mwa anthu otama dzina la Chauta mopemba.

Ankalira kwa Chauta Iye nkumaŵayankha.

7 Eks. 33.9 Ankalankhula nawo mu mtambo woima kuti njo.

Iwo ankasunga mapangano ndi malangizo

amene Iye adaŵapatsa.

8Inu Chauta, Mulungu wathu, munkaŵayankha,

munali Mulungu woŵakhululukira,

komabe wolanga ntchito zao zoipa.

9Tamandani Chauta, Mulungu wathu,

mpembedzeni ku phiri lake loyera.

Chauta, Mulungu wathu, ndi woyera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help