Mphu. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Munthu woopa Ambuye, tsoka silimgwera,

nthaŵi zonse Ambuye adzampulumutsa ku mavuto.

2Munthu wanzeru sadana ndi Malamulo.

Koma munthu wosakhulupirika ali ngati

ngalawa pakati pa namondwe.

3 Eks. 28.30; Mphu. 45.10 Munthu wanzeru amakhulupirira Malamulo,

ndipo kwa iye malamulowo ngokhulupirika

ngati mau olosa.

4Ukonzeretu zimene ukalankhule,

ndipo anthu adzamvetsera.

Ukumbukire bwino zimene udaphunzira, usanayankhe.

5Maganizo a chitsiru amakhala ngati mkombero wa ngolo,

maganizo ake amazungulira ngati njinga.

6Bwenzi wamchedzera ali ngati kavalo wakuthengo

amene amadzuma womkwera aliyense, ngakhale akhale yani.

Za kusiyana kwa anthu

7Bwanji tsiku lina limakhala labwino koposa linzake,

pamene dzuŵa limapereka kuŵala kolingana chaka chathunthu.

8Amasiyana chifukwa Ambuye adafuna choncho.

Ndiwo amene adasankhula nyengo ndi masiku achikondwerero.

9Masiku ena adaŵakweza ndi kuŵayeretsa,

koma ena adaŵasunga ngati masiku wamba.

10Anthu onse amachokera ku nthaka,

ndipo Adamu adapangidwa ndi dothi lam'nthaka.

11Mwa nzeru zao Ambuye adaika kusiyana pakati pa anthu,

makhalidwe ao adaŵapanga osafanana.

12Ena adaŵadalitsa ndi kuŵakweza,

ena adaŵayeretsa ndi kuŵaika pafupi nawo.

Koma ena adaŵatemberera ndi kuŵapeputsa,

adaŵatsitsa m'malo mwao.

13Dothi likakhala m'manja mwa mmisiri wake,

iye amaumba nalo chimene akufuna.

Chimodzimodzinso anthu m'manja mwa Mlengi,

amaŵapatsa zinthu monga Iye akufunira.

14Ubwino uli poyang'anana ndi kuipa,

moyo uli poyang'anana ndi imfa.

Chonchonso munthu wochimwa ali poyang'anana

ndi munthu wosamala za Mulungu.

15Yang'anani ntchito zonse za Mulungu

Wopambanazonse:

mudzaona kuti adazipanga ziŵiriziŵiri,

china chosiyana ndi chinzake.

16Ine ndidakhala wotsirizira kudzagwira ntchito.

Ndinali ngati wokunkha pambuyo pa anthu

othyola mphesa.

17Koma ndi madalitso a Ambuye ndidakhala wopambana,

motero nanenso ndidadzaza mopondera mphesa

ngati ena onse.

18Zindikirani kuti ntchitoyi sindidaigwire

chifukwa cha ine ndekha,

koma chifukwa cha onse ofuna kuphunzira.

19Tsono mundimvere, inu amene muli akuluakulu

pakati pa anthu;

tcherani khutu, inu atsogoleri a mpingo.

Za kudziimira pa wekha

20Pa moyo wako wonse usalole kuti wina akulamulire,

ngakhale akhale mwana wako,

mkazi wako, bwenzi lako kapena mbale wako.

Usapatse wina aliyense chuma chako,

kuwopa kuti mwina ungasinthe maganizo

nkumuuza kuti akubwezere.

21Nthaŵi yonse uli ndi moyo ndipo ukadapumabe,

usadzipereke mu ulamuliro wa wina aliyense.

22Ndi bwino kuti ana ako azigonera pa iwe

kupambana kuti iwe uzigonera pa ana ako.

23Ukhale wodzilamulira wekha pa zonse

zimene umachita,

usalole kuti mbiri yako iipe.

24Pamene masiku a moyo wako adzakhala pafupi kutha,

pa nthaŵi imene uzikamwalira,

pamenepo udzagaŵe chuma chako.

Za akapolo

25Udzu, ndodo ndi katundu ndizo zoyenera bulu.

Chakudya, mwambo ndi ntchito ndizo zofunikira akapolo.

26Uzimgwiritsa ntchito kapolo wako,

ndipo udzapeza mtendere mu mtima.

Ukangomlekerera osampatsa ntchito,

adzayamba kufuna ufulu wake.

27Goli ndi nsinga zimaŵeramitsa khosi ng'ombe.

Kapolo woipa amamzunza ndi matangadza.

28Umpatse ntchito kuti asamangokhala,

chifukwa ulesi umaphunzitsa munthu makhalidwe oipa.

29Mpatse ntchito pakuti ndiye chinthu chomuyenera,

akapanda kukumvera, ummange ndi maunyolo.

30Koma usakhale wankhalwe ndi munthu wina aliyense,

kapena kuchita kalikonse kosalungama.

31Ngati uli ndi kapolo, umsunge ngati mnzako,

chifukwa udamgula ndi magazi.

Ngati uli ndi kapolo, umsunge ngati mbale wako,

poti umamsoŵa monga umadzisoŵera mwiniwakewe.

Ukamamzunza, iye nkuthaŵa,

kodi udzadzera njira iti kuti udzampeze?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help