Eks. 28 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zovala za ansembe(Eks. 39.1-7)

1“Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

2Umsokere mkulu wako Aroni zovala zopatulika, kuti aziwoneka wolemerera ndi wolemekezeka.

3Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaŵapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zozivala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga.

4Zovala zimene udzasokezo ndi izi: chovala chapachifuwa, chovala cha efodi, mkanjo, mwinjiro wopetedwa bwino, nduŵira ndi lamba. Asoke zovala zopatulikazo za mbale wako Aroni ndi za ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira.

5Zovala zimenezi anthu alusowo azisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

6Efodi aisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.

7Idzakhale ndi tizikwewo tam'mapewa tiŵiri tosokerera ku nsonga zake ziŵiri, tomangira efodiyo.

8Padzakhalenso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso adzakhale wa nsalu ya golide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

9Utenge miyala iŵiri ya onikisi, ndipo ulembepo maina a ana a Israele.

10Pa mwala umodzi ulembepo maina asanu ndi limodzi, ndipo pa mwala winawo uchitenso chimodzimodzi. Ulembe mainawo motsatana malinga nkubadwa kwa ana a Israelewo.

11Maina aowo uŵalembe mozokota pa miyala iŵiriyo, potsata luso la mmisiri wozokota miyala. Ndipo miyalayo uiike m'zoikamo zake zagolide.

12Uike miyala iŵiri imeneyi pa tizikwewo tam'mapewa ta efodi, ngati chikumbutso cha ana a Israele. Mwa njira imeneyi, Aroniyo azidzanyamula pa mapewa mainawo, ndipo Chauta azidzaŵakumbukira iwowo.

13Upangenso zoikamo zonga maluŵa agolide,

14ndiponso maunyolo aŵiri a golide wokoma, opotedwa ngati zingwe, amene udzaŵalumikize ku zoikamozo.

Chovala chapachifuwa(Eks. 39.8-21)

15“Tsono usoke chovala chapachifuwa, chopetedwa mwaluso, chomavala poweruza. Mapangidwe ake akhale ngati a efodi, ndiye kuti a nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

16Kukula kwake kukhale kofanana mbali zonse, ndipo chikhale chopinda paŵiri. M'litali mwake chikhale masentimita 23, muufupi mwake chimodzimodzi.

17Usokererepo mizere inai ya miyala. Pa mzere woyamba pakhale miyala ya rubi, topazi ndi garaneti.

18Pa mzere wachiŵiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi.

19Pa mzere wachitatu pakhale miyala ya yasinti, agate ndi ametisiti.

20Pa mzere wachinai pakhale miyala ya berili, onikisi ndi jasipere, ndipo zonsezo ziikidwe m'zoikamo zagolide.

21Miyala imeneyi ikhalepo khumi ndi iŵiri, potsata maina a mafuko a Aisraele. Miyalayo izokotedwe ngati zidindo, uliwonse ukhale ndi dzina la fuko limodzi.

22Upange timaunyolo ta golide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota mwaluso ngati maukufu.

23Upangenso mphete ziŵiri, ndipo uzilumikize pa ngodya zam'mwamba za chovala chapachifuwa.

24Umange zingwe zagolide ziŵiri ku mphete ziŵirizo.

25Ndipo nsonga zake zina ziŵiri za zingwezo uzimange ku zoikamo zake zija.

26Upangenso mphete ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zam'munsi za chovala chapachifuwa, ku nsonga yake yam'kati, pafupi ndi chovala cha efodi chija.

27Upangenso mphete zina ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize cham'munsi, kutsogolo kwake kwa malamba aŵiri a pa mapewa a efodi, pafupi ndi misoko, pa lamba wolukidwa mwaluso uja.

28Tsono ulumikize mphete za chovala chapachifuwacho ku mphete za chovala cha efodi chija ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba wolukidwa mwaluso uja, ndipo chovala chapachifuwa chilumikizike bwino ku chovala cha efodi.

29Ndipo Aroni akamaloŵa m'malo opatulika, azivala chovala chapachifuwa cholembedwa maina onse a ana a Israele, kuti Chauta azidzaŵakumbukira.

30Num. 27.21; Deut. 33.8; Eza. 2.63; Neh. 7.65 M'chovala chapachifuwacho uziikamo zinthu zoyera za Chauta zotchedwa Urimu ndi Tumimu, kuti zimenezo zikhale pa chifuwa cha Aroni akamapita kwa Chauta. Motero Aroni akakhala pamaso pa Chauta, nthaŵi zonse adzakhala ndi zomthandiza kuweruza bwino mpingo wa Israele.

Zovala zina za ansembe(Eks. 39.22-31)

31“Upange mkanjo wa nsalu yobiriŵira, wophimba chovala cha efodi chija.

32Pakati pake pa mkanjowo usiye chiboo chopisapo mutu. Chiboo chimenechi chikhale chosokerera mwamphamvu mozungulira monse, ngati khosi la malaya, kuti mkanjowu usang'ambike.

33Mphu. 45.9Pa mpendero wapansi wa mkanjowo, upange zinthu zonga makangaza. Zikhale za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, kuzungulira mkanjo wonsewo. Pakati pa makangazawo pakhale timabelu tagolide.

34Choncho pakhale khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo.

35Tsono Aroni azivala mkanjowo pamene akutumikira zaunsembe. Akamaloŵa m'malo opatulika pamaso pa Chauta kapena pochoka kumeneko, liwu la timabeluto lizidzamveka, kuti asafe.

36“Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’

37Ulimange ndi kamkuzi kobiriŵira pa nduŵira ya Aroni, ndipo likhale cha kutsogolo kwa nduŵirayo.

38Likhaledi pamphumi pake pa Aroni, motero asenze iye yemwe cholakwa chilichonse cha pa zopereka zimene Aisraele amazipatulira Chauta. Kuti Chauta alandire zopereka za anthuzo, Aroni azivala duŵali pa nduŵira yake nthaŵi zonse.

39“Umsokerenso Aroni mwinjiro wa bafuta wokoma, ndipo umpangire nduŵira ya bafuta wokoma, ndiponso lamba wopetedwa mokongola.

40“Ana a Aroni, uŵasokere miinjiro, malamba ndi nduŵira, kuti azisiyana ndi anthu ena, ndipo iwowo aziwoneka olemerera ndi olemekezeka.

41Zovala zimenezi uveke mbale wako Aroni ndi ana ake. Tsono uŵadzoze, uŵapatse udindo ndi kuŵapatula, kuti akhale ansembe onditumikira.

42Uŵasokere akabudula ofika m'ntchafu, kuti asamaonetse maliseche.

43Aroni ndi ana ake azivala zimenezi nthaŵi zonse akamapita ku chihema chamsonkhano kapena ku guwa, kukanditumikira ku malo opatulika aja, kuwopa kuti angachimwe ndipo angafe. Lamulo limeneli, lonena za Aroni ndi zidzukulu zake, ndi lokhazikika mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help