Eks. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chiyambi cha Paska

1 Lev. 23.5; Num. 9.1-5; 28.16; Deut. 16.1, 2 Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m'dziko lija la Ejipito kuti,

2“Mwezi uno udzakhala mwezi wanu woyambira chaka.

3Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi.

4Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja aŵiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiŵerengero cha anthu odya nyamayo, modziŵa m'mene munthu mmodzi angadyere.

5Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi.

6Mumsunge mpaka tsiku la 14 la mwezi, pamene khamu lonse la Aisraele lidzaphe nyama zaozo madzulo ndithu.

7Tsono adzatengeko magazi a nyamayo ndi kuwaza pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, ndi pamwamba pa chitseko cha nyumba m'mene akadyeremo nyamayo.

8Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba.

9Musaidye yaiŵisi kapena yophika, koma muwotche yonse pamodzi ndi mutu wake womwe, miyendo ndi zonse zam'kati.

10Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe.

11Kudya kwake, muzikadya motere: Mudzavale zaulendo, nsapato zanu zili kuphazi, ndodo zili kumanja. Mudzadye mofulumira. Limeneli ndilo tsiku la Paska ya Chauta.

12Usiku umenewo, Ine ndidzapita m'dziko la Ejipito ndipo m'dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta.

13Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.

14 Eks. 23.15; 34.18; Lev. 23.6-8; Num. 28.17-25; Deut. 16.3-8 “Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”

Kukhazikitsa chikondwerero cha buledi wosafufumitsa

15Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele.

16Pa tsiku loyamba, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, muzidzachita msonkhano wachipembedzo. Musadzagwire ntchito pa masiku amenewo, koma chakudya chokha choti aliyense adye, mudzatha kukonza.

17Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.

18Muzidzadya buledi wosafufumitsa kuyambira madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba, mpaka madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.

19Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe.

20Musadye chilichonse chofufumitsa, ndipo ku nyumba zanu zonse muzidzangodya buledi wosafufumitsa.”

Paska yoyamba

21Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo.

22Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa.

23Ahe. 11.28 Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni.

24Muziŵamvera malamulo ameneŵa inuyo ndi ana anu mpaka muyaya.

25Ndipo mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, monga momwe adalonjezera, muzidzasunga mwambo umenewu.

26Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’

27Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.

28Aisraele adapita, ndipo adamvera zimenezo. Adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni.

Imfa ya ana achisamba

29 Eks. 4.22, 23 Pakati pa usiku, Chauta adapha ana onse achisamba m'dziko la Ejipito. Adayambira mwana wachisamba wa Farao amene ankayembekezeka kuloŵa ufumu wake, mpaka ana a akaidi a m'nyumba zamdima za m'ndende. Ana onse oyamba kubadwa a nyama adaphedwanso ndithu.

30Farao ndi nduna zake zonse, pamodzi ndi Aejipito onse, adadzuka pakati pa usiku, ndipo m'dziko lonse la Ejipito munali maliro okhaokha, chifukwa panalibe banja lopanda mwana wakufa.

31Usiku womwewo Farao adaitana Mose ndi Aroni, ndipo adaŵalamula kuti, “Inu pamodzi ndi Aisraele onse, fulumirani, mutuluke. Asiyeni anthu anga, pitani mukapembedze Chauta monga momwe mudanenera.

32Mutenge nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zanu zomwe, monga momwe mudanenera, ndipo muchoke. Mukapemphere kuti nanenso andidalitseko.”

33Aejipito adafulumizitsa anthu kuti achoke m'dzikomo, namanena kuti, “Tifatu tonsefe.”

34Motero anthuwo adanyamula pa mapewa ao ufa wa buledi wokandiratu asanathire chofufumitsira, pamodzi ndi mbale zokandiramo buledi zili zokulunga m'nsalu.

35Eks. 3.21, 22 Ndiponso Aisraele anali atachita monga momwe Mose adaaŵauzira. Adaapempha kwa Aejipitowo zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala.

36Chauta adasandutsa Aejipito aja kuti akhale okoma mtima, ndipo anthuwo adapatsa Aisraele zonse zimene ankapempha. Motero Aisraele adalandako chuma cha Aejipito aja.

Aisraele atuluka ku Ejipito

37Tsono Aisraele adanyamuka ulendo kuchoka ku Ramsesi kupita ku Sukoti. Anthu aamuna analipo zikwi 600, osaŵerenga akazi ndi ana.

38Panalinso gulu lalikulu la anthu ena, ndiponso nkhosa, mbuzi pamodzi ndi ng'ombe zomwe.

39Adaphika mitanda ya buledi wosafufumitsa wa ufa wokandiratu, yomwe adachoka nayo ku Ejipito kuja. Ufa wabuledi wokandiratuwo unali wosathira chofufumitsira chifukwa anali atapirikitsidwa mwadzidzidzi ku Ejipito kuja. Panalibe nthaŵi yophikira chakudya chao cha kamba.

40 Gen. 15.13; Aga. 3.17 Aisraele adakhalako zaka 430 ku Ejipito kuja.

41Pa tsiku lomwe zaka 430 zinkatha, magulu onse a Chauta adachokako ku Ejipito.

42Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera.

Za malamulo a Paska

43Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Malamulo ake a Paska ndi aŵa: Mlendo aliyense asadyeko.

44Kapolo aliyense wochita kugulidwa angadyeko, koma atayamba waumbalidwa.

45Mlendo kapena wantchito wanu aliyense asadyeko.

46Num. 9.12; Yoh. 19.36 Muzidyera m'nyumba imodzi, musatuluke nayo panja nyamayo, ndipo musaphwanye mafupa ake.

47Mtundu wonse wa Aisraele uzichita mwambo umenewu.

48Mlendo akakhala pakati panu, namafuna kuti achite nao mwambo wa Paska ya Chauta, muziyamba mwaumbala amuna onse am'banjamo. Pambuyo pake angathe kuloŵa ndi kumachita nao mwambowo. Iyeyo muzimuyesa ngati mbadwa yeniyeni ya Israele. Koma wosaumbalidwa asadyeko.

49Lamulo limeneli ndi la mbadwa yeniyeni ya Israele, ndiponso la mlendo woumbalidwa amene ali pakati panu.”

50Aisraele onse adamveradi zimenezi, ndipo ankachitadi zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni.

51Pa tsiku lomwelo ndi pamene Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito mwa magulumagulu ao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help