1Nthaŵi imeneyo anthu a mu mzinda woyera anali ndi mtendere wonse, ndipo ankasunga bwinobwino Malamulo onse a Mulungu, chifukwa Oniyasi, mkulu wa ansembe, anali munthu wopemphera ndi wodana ndi zoipa.
2Ngakhale mafumu omwe ankalemekeza malowo ndi kukulitsa ulemu wa Nyumba ya Mulungu, popereka mphatso zokoma.
3Ndi Seleuko yemwe, mfumu ya ku Asiya, ankatulutsa ndalama m'bokosi lake zoti alipirire zonse zofunikira ku nsembe zosiyanasiyana.
4Tsiku lina munthu wina dzina lake Simoni wa fuko la Benjamini, amene anali mkulu woyendetsa zinthu ku Nyumba ya Mulungu, adatsutsana ndi mkulu wa ansembe pa za malamulo a msika wamumzinda.
5Popeza kuti sadathe kutsutsa Oniyasi, adanka kwa Apoloniyo mwana wa Traseo, amene pa nthaŵiyo anali bwanamkubwa wa ku Celesiriya ndi ku Fenisiya.
6Simoni adamuuza kuti m'bokosi la chuma cha ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu munali chuma chobisika ndi chosaŵerengeka, chosafunikira ku nsembe, ndipo choncho kunali kotheka kuchipereka chonsecho kwa mfumu.
7Apoloniyo adapita kwa mfumu, nakaidziŵitsa za chuma chimene adaanenacho. Pamenepo mfumu idasankhula Heliodoro, nduna yake yaikulu, namtuma ndi lamulo loti akachilande chuma chambiricho.
Ulendo wa Heliodoro ku Yerusalemu8Heliodoro adanyamuka nthaŵi yomweyo, nachita ngati akufuna kukayendera mizinda ya ku Celesiriya ndi ya ku Fenisiya, koma kwenikweni ankafuna kuchita cholinga cha mfumu.
9Atafika ku Yerusalemu, mkulu wa ansembe ndi anthu amumzinda adamlandira mwaufulu. Pamenepo iyeyo adakambira Oniyasi zimene adaamva, namufotokozera cholinga cha ulendo wake. Kenaka adamufunsa ngati zinalidi choncho.
10Tsono mkulu wa ansembe adamuyankha kuti m'bokosi la chuma munali ndalama zothandiza azimai amasiye ndi ana amasiye.
11Munalinso ndalama zina za Hirkano, mwana wa Tobiyasi, munthu wotchuka kwambiri. Motero zidadziŵika kuti mau a Simoni uja anali mabodza okhaokha. Zoona zinali zakuti chuma chonse pamodzi chinali cha makilogramu 1,300 a siliva ndi makilogramu 6,000 a golide basi.
12Adaonjezanso kuti kunali kosayenera konse kuŵavutitsa amene ankakhulupirira kupatulika, kuyera ndi kusakhudzika kwake kwa Nyumba ya Mulungu yolemekezeka pa dziko lonse lapansi.
13Koma Heliodoro potsata malamulo amene mfumu adaampatsa, adangoumirira ndithu kuti chumacho chidaayenera kuloŵa m'bokosi la mfumu.
14Adasankhuliratu tsiku lodzaŵerenga chumacho, ndipo adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, kuti adziwonere yekha. Poona zimenezi, anthu onse amumzinda adavutika kwambiri.
15Ansembe adadzigwetsa pansi chafufumimba ku guwa atavala zaunsembe, ndipo adapemphera Mulungu amene adaaŵapatsa malamulo onena za ndalama zoikiza kuti aziŵasungira bwino amene ankaikamowo.
16Amene adaona nkhope ya mkulu wa ansembe adamva chisoni mumtima mwao, chifukwa nkhope yake ndi kutumbuluka kwa maonekedwe ake kudaasonyeza nkhaŵa ya mumtima mwake.
17Nthumanzi ndi kunjenjemera zidamugwira, ndipo chisoni cha mumtima mwake chidaoneka kwa anthu onse ompenya.
18Anthu ambiri a ku Yerusalemu adatuluka m'nyumba mwao kuti apemphere poyera onse pamodzi, popeza kuti mwina malo oyerawo adzanyozeka.
19Azimai adangoti balala m'miseu, atangomanga ziguduli m'chiwuno, maŵere ali pamtunda. Anamwali amene ankangokhala m'nyumba mwao adathamanga, ena ku zipata, ena pamwamba pa chipupa, ndipo ena ankangosuzumira pa windo.
20Onse adakweza manja kumwamba nkumapemphera.
21Madandaulo a anthu onse ndi nkhaŵa ya mkulu wa ansembe zinali zomvetsa chisoni.
Chilango cha Heliodoro22Pamene Ayuda ankapemphera kwa Ambuye amphamvuzonse kuti aŵasungire bwino chuma chao onse amene adaaikizamo,
23Heliodoro adayambako kuchita zimene adaakonzera.
24Atangofika ndi atetezi ake pafupi ndi bokosi la chuma, Ambuye Mfumu ya mizimu yonse ndi Mwini ulamuliro wonse adachita chozizwitsa choopsadi, ndipo onse aja amene sadaope kuloŵa m'malowo, adazizwa ndi mphamvu za Mulungu, ndipo adafooka ndi kuchita mantha kwambiri.
25Pamaso pao padaoneka kavalo wovala zakaso ndipo wokwerapo wake anali ndi nkhope yoopsa. Kavaloyo adalumphira Heliodoro mwamphamvu nkumutchaya ndi mapazi ake. Wokwerapo wake anali atavala zankhondo zagolide.
26Ndipo pafupi ndi Heliodoroyo padaonekanso anyamata aŵiri amphamvu kwambiri ndi okongola kwabasi, ovala nsalu zakaso. Adadzaima pambali pake, wina kumanja wina kumanzere, namamkwapula kosalekeza ndi kummenya kwambiri.
27Heliodoro adagwa pansi, m'maso mwake nkuchita chidima. Anthu ake adamuika m'machira nachoka naye.
28Posachedwa pomwepa munthu ameneyu adaaloŵa m'nyumba ya chuma, ali ndi gulu lalikulu la atetezi ake, koma tsopano adachita kumnyamula, osathanso kuyenda yekha. Choncho mphamvu za Mulungu zidaonekera poyera.
29Poona munthu wolangidwa ndi mphamvu za Mulunguyo ali thasa, osalankhula ndiponso osayembekeza kuchira,
30Ayuda adayamika Mulungu amene adaonetsa motere ulemerero wa malo ake oyera. Tsono Nyumba ya Mulungu imene posachedwapa inali yodzaza ndi mantha ndi nkhaŵa, tsopano inali yodzaza ndi chimwemwe ndi chikondwerero, chifukwa cha kudziwonetsa kwa Ambuye amphamvuzonse.
31Abwenzi ena a Heliodoro adapempha Oniyasi, mkulu wa ansembe, kuti apemphere kwa Wopambanazonse kuti munthu amene anali thasa ali pafupi kufayo, amusiye wamoyo.
32Tsono mkulu wa ansembe, poopa kuti mwina mfumu ingaganize kuti Ayuda adamchita Heliodoro zoipa, adapereka nsembe kuti munthuyo achire.
33Pamene mkulu wa ansembe onse ankapereka nsembe yopepesera tchimo la Heliodoro, anyamata aŵiri omwe aja, atavala zonzija, adamuwonekeranso Heliodoro namuuza kuti, “Uthokoze kwambiri Oniyasi, mkulu wa ansembe onse, popeza kuti Ambuye akusungira moyo wako chifukwa cha iyeyo.
34Ndipo iwe amene walangidwa chotere, uzikalalika mphamvu zazikulu za Mulungu pakati pa anthu.” Atanena zimenezo, anyamata aja adazimirira.
Heliodoro atembenuka mtima35Heliodoro adapereka nsembe kwa Ambuye, naŵalonjeza zambiri chifukwa chopulumutsa moyo wake. Kenaka adatsazikana ndi Oniyasi mwaulemu, napita ndi ankhondo ake kwa mfumu.
36Ankachita umboni pamaso pa onse pakulalika za ntchito za Mulungu Wopambanazonse zimene iye yemwe anali ataziwona ndi maso ake.
37Tsono mfumu idafunsa Heliodoro kuti aidziŵitse munthu wina woyenera kumtumanso ku Yerusalemu. Iyeyo adayankha kuti,
38“Ngati muli ndi munthu wina wodana nanu kapena wopandukira boma lanu, mutume ameneyo kumeneko, ndipo adzabwerera atamkwapula kwambiri, ngatitu akapulumuke, chifukwatu kumeneko kuli mphamvu za Mulungu.
39Iye amene kwao nkumwamba amayang'anira malowo, ndipo amaŵatchinjiriza. Onse opitako ndi maganizo oipa, amaŵamenya ndi kuŵapha.”
40Imeneyi ndiyo mbiri ya Heliodoro ndi kutetezedwa kwa bokosi la chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.
Simoni asinjirira OniyasiWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.