Zek. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta aweruza adani a YudaMau olosa

1

8Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo,

kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo.

Palibe adani amene adzaŵapambane,

pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.”

Mfumu yamtendere

9 Mt. 21.5; Yoh. 12.15 Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni.

Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu.

Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu.

Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani.

Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu,

bulu wake kamwana tsono.

10 Mas. 72.8 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu

ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu.

Uta wankhondo adzauthyola.

Mfumu yanu idzachititsa mtendere

pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina

mpaka ku nyanja ina,

ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate

mpaka ku mathero a dziko lapansi.

11 Eks. 24.8 Chauta akuti,

“Tsono kunena za inu,

chifukwa cha chipangano changa ndi inu,

chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza,

ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi

anthu anu amene ali ngati akapolo.

12Bwererani ku linga lanu lolimba,

inu akapolo amene tsopano muli ndi chikhulupiriro.

Lero ndi tsiku limene ndikulengeza

kuti ndidzakubwezerani zabwino moŵirikiza.

13“Ndidzakoka Yuda ngati uta wanga,

Efuremu adzakhala ngati muvi wake.

Ndidzatenga ana ako, iwe Ziyoni,

kuti alimbane ndi ana ako, iwe Grisi;

ndidzakugwira ngati lupanga la wankhondo wamphamvu.”

14Tsono Chauta adzaonekera anthu ake,

ndipo mivi yake adzaiponya ngati zing'aning'ani.

Ambuye Chauta adzaliza lipenga,

ndipo adzayenda m'kamvulumvulu wochokera kumwera.

15Chauta Wamphamvuzonse adzakhala chishango chao.

Iwowo adzapambana ndi kugonjetsa adani ao

poponya miyala chabe.

Adzamwa magazi ao nkumafuula ngati okhuta vinyo.

Magaziwo adzachita kuyenderera ngati magazi a nsembe,

othira ndi mkhate pa guwa popembedza.

16Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa,

pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa.

M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira

ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu.

17Dzikolo lidzakhaladi lokongola kwambiri.

Tirigu adzalimbitsa anyamata,

ndipo vinyo watsopano adzakometsa anamwali.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help