1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2Yer. 31.29 “Chifukwa chiyani anthu a ku Israelenu mumakonda kubwerezabwereza mwambi uja wakuti, ‘Nkhuyu zodya akulu zidapota ndi ana omwe?’
3Ndithu, pali ine ndemwe wamoyo, mwambi umenewu simudzaunenanso ku Israele.
4Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
5“Tiyese kuti pali munthu wabwino amene amatsata malamulo ndi kuchita zabwino.
6Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba.
7Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa.
8Sakongoza ndalama kuti apezepo phindu kapena kulandira chiwongoladzanja. Amadziletsa kuchita zoipa, ndipo sachita mokondera pogamula milandu ya anthu.
9Lev. 18.5Amatsata malangizo anga, ndipo amamvera malamulo anga mokhulupirika. Munthu wotereyu ndi wolungama, adzakhala ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
10“Mwina munthu wotero nkubala mwana amene ntchito yake nkuba ndiponso kupha anthu.
11Iye amachita zambiri zimene bambo wake sadachitepo. Amadyera nao ku zitunda zachipembedzo, amaipitsa mkazi wa munthu wina,
12amazunza osoŵa ndi osauka. Amaba, sabwezera chigwiriro cha munthu wangongole. Amatembenukira ku mafano, namachita zonyansa.
13Amakongoza kuti apezepo phindu, ndipo kuti alandire chiwongoladzanja. Kodi munthu wotereyu nkukhala ndi moyo? Ai ndithu, sadzakhala ndi moyo. Chifukwa adachita zoipa zonsezi, adzaphedwa, ndicho chilango chomuyenerera.
14“Mwina mwake munthu woipa uja nkubala mwana amene aona machimo a bambo wake. Amaona, koma satsanzirako. Sadyera nao ku zitunda zachipembedzo.
15Sapembedza mafano a ku Israele, saipitsa mkazi wa munthu wina,
16sazunza munthu wina aliyense, satenga chigwiriro ndipo saaba. Koma amadyetsa anjala ndi kuveka ausiŵa.
17Amakana kuchita zoipa, sakongoza kuti apezepo phindu kapena kuti alandire chiwongoladzanja. Amatsata malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu woteroyo sadzafera zolakwa za bambo wake. Adzakhala ndi moyo.
18Koma bambo wake, popeza kuti adachimwa pozunza anthu ena ndi kubera mbale wake ndiponso kuŵachita zoipa anansi ake, adzafera zoipa zakezo.
19“Mwina mungathe kufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha zolakwa za bambo wake?’ Mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa choti nthaŵi zonse ankachita zolungama ndi zokhulupirika, ndipo ankamvera malamulo anga onse mosamala.
20Deut. 24.16Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake.
21“Munthu wochimwa akaleka machimo ake amene ankachita, namamvera malamulo anga onse, ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndithudi ameneyo adzakhala ndi moyo, sadzafa.
22Zoipa zake zonse zidzakhululukidwa. Adzakhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zolungama.
23Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi imfa ya munthu woipa Ine ndimakondwera nayo? Iyai, koma ndikadakonda kuti woipa aleke njira zake zoipa ndi kukhala ndi moyo.
24“Koma munthu wabwino akasanduka woipa, namachita zonyansa za mitundu yonse zimene anthu amachita, kodi munthu woteroyo nkukhala ndi moyo? Iyai, ntchito zake zonse zabwino sizidzakumbukika. Wapalamula, wachimwa, adzafa basi.
25Koma inu mumati, ‘A! Zimene Ambuye amachitazi nzopanda chilungamo.’ Tamvani tsono Aisraele inu: Kani zochita zanga ndiye zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene zili zosalungama?
26Ngati munthu wabwino aleka kuchita zoyenera, namachita zoipa, adzafa chifukwa cha zoipa zakezo.
27Komanso munthu woipa akaleka zoipa zake, namachita zoyenera, adzapulumutsa moyo wake.
28Poti adazindikira kuipa kwa zolakwa zake, nazileka, ndiye kuti adzakhala ndi moyo, sadzafa.
29Komabe Aisraele akunena kuti zochita za Ambuye nzosalungama. Pepani, Aisraele inu, ndinu amene mumachita zosalungama, osati Ine.
30“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
31Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele?
32Lun. 1.13Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.