Chiv. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za mai ndi chinjoka

1Pambuyo pake kudaoneka chizindikiro chachikulu kuthambo: mai atavala dzuŵa, mapazi ake ataponda pa mwezi, pamutu pake pali chisoti chaufumu cha nyenyezi khumi ndi ziŵiri.

2Maiyo anali ndi pathupi, ndipo pa nthaŵi yochira adalira nako mokuwa kupweteka kwa kubala.

3 Dan. 7.7 Kudaonekanso chizindikiro china kuthambo: chinjoka chachikulu, chofiira, cha mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi; pa mutu uliwonse chitavala chisoti chaufumu.

4Dan. 8.10Ndi mchira wake chidakokolola chimodzi mwa zigawo zitatu za nyenyezi zakuthambo, nkuzigwetsa pa dziko lapansi. Chinjokacho chidadzaimirira pamaso pa mai uja amene anali pafupi kubala mwana, kuti akangobadwa mwanayo, chimudye.

5Yes. 66.7; Mas. 2.9Maiyo adabala mwana wamwamuna, woyenera kudzalamulira anthu a mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo. Mwanayo adalandidwa kumanja kwa mai wake kupita naye kwa Mulungu ndi ku mpando wake wachifumu.

6Apo mai uja adathaŵira ku chipululu. Kumeneko Mulungu adaakonzeratu malo ake, kuti akasamalidweko masiku 1,260.

7 Dan. 10.13, 21; 12.1; Yuda 1.9 Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo,

8koma onsewo adagonjetsedwa, mwakuti adataya malo ao Kumwamba.

9Gen. 3.1; Lk. 10.18Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.

10 Yob. 1.9-11; Zek. 3.1 Pamenepo ndidamva mau amphamvu Kumwamba akunena kuti,

“Tsopano Mulungu wathu watipulumutsa.

Waonetsa mphamvu zake ndi ufumu wake.

Tsopano Wodzozedwa uja waonetsa ulamuliro wake.

Woneneza abale athu uja wagwetsedwa pansi,

amangokhalira kuŵaneneza kwa Mulungu wathu

usana ndi usiku.

11Abale athuwo adamgonjetsa

ndi magazi a Mwanawankhosa uja,

ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni.

Iwo adadzipereka kotheratu,

kotero kuti sadaope ngakhale kufa.

12Choncho kondwerani inu,

Dziko la Kumwamba, ndi onse okhalamo.

Koma muli ndi tsoka, inu dziko lapansi ndi nyanja,

pakuti Satana adatsikira kwa inu, ali wokalipa kwambiri,

chifukwa wadziŵa kuti yangomutsalira nthaŵi pang'ono.”

13Tsono chinjoka chija chitaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chidayamba kumpirikitsa mai uja amene anali atabala mwana wamwamuna.

14Dan. 7.25; 12.7Koma maiyo adapatsidwa mapiko aŵiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athaŵire ku malo ake aja akuchipululu. Kumeneko adzasamalidwa zaka zitatu ndi hafu, kuwopa kuti chinjoka chija chingamuwone.

15Pamenepo chinjokacho chidalavulira mai uja madzi ochuluka ngati mtsinje, kuti amkokolole.

16Koma dziko lapansi lidamthandiza maiyo: lidayasama nkuumeza mtsinje umene chinjoka chija chidaalavula.

17Apo chinjokacho chidamupsera mtima kwambiri mai uja, nkungochokapo kuti chikayambane ndi ana ena onse a maiyo, ndiye kuti anthu otsata malamulo a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Motero chidakaimirira pambali pa nyanja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help