1Tsono Bilidadi wa ku Suki adayankha kuti,
2“Kodi iwe Yobe, ukhala mpaka liti ukufunafuna zonena?
Ingokhala chete, umvetsere, ndipo ife tilankhula.
3Chifukwa chiyani ukutiyesa opusa ngati ng'ombe?
Chifukwa chiyani tikuwoneka ngati
opanda nzeru m'maso mwako?
4Iwe ukungodzipweteka ndi mkwiyo wako.
Kodi dziko lapansi lidzasanduka bwinja
chifukwa choti iweyo uli wokwiya?
Kodi thanthwe nkudzachotsedwa pamalo pake,
kuti likukondweretse iweyo?
5 Yob. 21.17 “Nyale ya munthu woipa yazima,
malaŵi a moto wake sakuŵalanso.
6Kuŵala kwa m'nyumba mwake kwasanduka mdima,
ndipo nyale ya pambali pake yazima.
7Kale ankayenda ndi mgugu, koma tsopano wakhumudwa.
Nzeru zake zomwe zamgwetsa.
8Mapazi ake omwe amloŵetsa mu ukonde, ndipo wakodwa.
Tsono kuti achokemo, wagweranso m'mbuna.
9Msampha wamkola mwendo,
ndipo khwekhwe lamgwira.
10Amtchera msampha pansi mobisika,
amtchera diŵa m'njira.
11Zoopsa zikumchititsa mantha pa mbali zonse,
zikumtsatira pambuyo pake.
12Adaali ndi mphamvu, koma tsopano ali ndi njala.
Tsoka likumdikira nthaŵi zonse.
13Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse,
miyendo yake, manja ake, zonse zaola.
14Amuchotsa m'nyumba mwake m'mene ankadalira.
Amkokera kwa Imfa, mfumu ya zoopsa zonse.
15M'nyumba mwake zake zonse zachotsedwamo,
awazamo sulufule, kuti aphe tizilombo ta matenda.
16Mizu yake ikuuma pansi,
nthambi zake zikufota.
17Sadzamkumbukiranso kwao kapena kwina kulikonse,
dzina lake lidzaiŵalika.
18Adzamchotsa m'dziko la amoyo ndi kumponya mu mdima,
adzampirikitsa pa dziko lapansi.
19Sadzaona zidzukulu m'banja mwake.
Sikudzaoneka ana otsala kumene ankakhalako.
20Anthu akuzambwe adabwa nalo tsoka lakelo,
anthu akuvuma nawonso akungopukusa mitu.
21Ndithu zimenezi ndizo zimagwera anthu oipa.
Kumeneku ndiye kutha kwake kwa anthu
osasamala za Mulungu.”
Yobe
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.