1 Sam. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Imfa ya Saulo ndi ana ake.(1 Mbi. 10.1-12)

1Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraelewo adathaŵa Afilisti, ndipo ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa.

2Afilistiwo adalondola Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikusuwa, ana a Saulo.

3Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa.

4Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke ndi kundipha.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.

5Wonyamula zida uja ataona kuti Saulo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake nafera naye limodzi.

6Motero Saulo adafa pamodzi ndi ana ake atatu, kudzanso munthu wonyamula zida zake, kuphatikizapo ankhondo ake ambiri, onsewo tsikulo.

7Aisraele amene anali tsidya lina la chigwa cha Yezireele, ndiponso amene anali tsidya lina la Yordani, ataona kuti anzao adathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake adafa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo.

8M'maŵa mwake Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake atatu pa phiri la Gilibowa.

9Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe.

10Tsono adaika zida zankhondo za Sauloyo m'nyumba yopembedzeramo Asitaroti, mulungu wao. Ndipo adakhomerera mtembo wake ku khoma la mzinda wa Betisani.

11Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zimene Afilisti adaamchita Saulo,

12amuna ena olimba mtima adanyamuka, ndipo adayenda usiku wonse, nakachotsa mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake ku khoma la Beteseani. Atabwerera ku Yabesi adatentha mitemboyo kumeneko.

13Pambuyo pake adatenga mafupa ao naŵakwirira patsinde pa mtengo wa mbwemba ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help