Ezek. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzalanga Yerusalemu

1Mzimu wa Mulungu udandinyamula kupita nane ku chipata chakuvuma cha Nyumba ya Chauta. Poloŵerapo panali anthu 25, ndipo pakati pa anthuwo ndidaona atsogoleri aŵa a anthu: Yazaniya mwana wa Azuri, ndi Pelatiya mwana wa Benaya.

2Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu aŵiri ameneŵa ndiwo amene amapangana zoipa nkumalangiza anthu zoipa mumzinda muno.

3Iwo amati, ‘Nthaŵi sinafike yoti nkumanga nyumba. Mzindawu uli ngati mphika umene uli pa moto, ifeyo tili ngati nyama imene ili mumphikamo.’

4Tsono iwe mwana wa munthu, ulose moŵadzudzula, ulose ndithu.”

5Pamenepo Mzimu wa Chauta udandigwira, ndipo udandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Inu a m'banja la Israele, ndikudziŵa zimene zili mumtima mwanu.

6Mwakhala mulikupha anthu ambiri mumzinda muno, ndipo mwaunjika mitembo yao m'miseu.’

7“Nchifukwa chake Ambuye Chauta akunena kuti, ‘Mitembo ya anthu ophedwa imene mwaika kumeneko, imeneyo ndiyo nyama. Mzindawu ndiwo mphika ndithu. Koma ndidzakutulutsanimo.

8Mukuwopa lupanga, tsono ndidzakugwetserani lupangalo.

9Ndidzakutulutsani mumzimdamo, ndidzakuperekani kwa anthu akudza kuti akulangeni.

10Inunso mudzafa ndi lupanga, ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

11Choncho mzindawo sudzakhalanso ngati mphika wokutetezani, ndipo simudzakhalanso ngati nyama yam'menemo ai. Ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele.

12Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Simudatsate malangizo anga, simudamvere malamulo anga. Koma mwakhala mukutsata malamulo a mitundu ya anthu okuzungulirani.’ ”

13Pamene ndinkalosa, nthaŵi yomweyo Pelatiya mwana wa Benaya adafa. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba nkufuula kuti, “Inu Ambuye Chauta, kodi mukufuna kuŵatheratu Aisraele onse otsala?”

Mulungu alonjeza za kubwerera kwa akapolo

14Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

15“Iwe mwana wa munthu, achibale ako, ndiye kuti abale ako, anzako a ku ukapolo, onse a m'banja la Israele, anthu okhala ku Yerusalemu akuŵanena kuti, ‘Onse aja amene adatengedwa ukapolo ali kutali ndi Chauta, dziko lino tsopano nlathu.’ ”

16“Nchifukwa chake uza anzako a ku ukapolo kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndine amene ndidaŵatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri. Pakali pano ndikuŵasungabe kumaiko kumene adatengedwako.”

17“Nchifukwa chake unene ndithu kuti Ine Chauta mau anga ndikuti, Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuŵasonkhanitsa pamodzi, kuchokera kumaiko kumene ndidaŵabalalitsa. Kenaka ndidzaŵapatsa dziko la Israele.

18Akadzaloŵa m'dzikomo, azidzachotsamo mafano onse oipa ndi onyansa.

19Ezek. 36.26-28 Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu.

20Motero adzatsata malamulo anga, adzasunga ndi kumvera malangizo anga. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.

21Koma amene mitima yao yazama m'zonyansa ndi zoipa zinazo, ndidzaŵalanga chifukwa cha zonse zimene adachita. Ndikutero Ine Chauta.”

Ulemerero wa Chauta uchoka ku Yerusalemu

22 Ezek. 43.2-5 Tsono akerubi aja adayamba kuuluka, mikombero ili m'mbali mwao, ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pa iwo.

23Ulemerero wa Chautawo udakwera ndi kusiya mzindawo, nukaima pa phiri chakuvuma kwake kwa mzindawo.

24Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu udandinyamula nukandifikitsa kwa akapolo ku dziko la Babiloni. Zonsezi zidachitika m'masomphenya, monga momwe Mzimu wa Mulungu udaandiwonetsera. Kenaka zinthu zimene ndinkaziwonazo zidayamba kuzimirira.

25Ndipo ndidaŵasimbira akapolo zonse zimene Chauta adaandiwonetsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help