Lev. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nsembe yopepesera kupalamula

1“Nsembe yopepesera kupalamula njoyera kopambana. Lamulo lake ndi ili:

2pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, azipheraponso nsembe yopepesera kupalamula, ndipo awaze magazi ake pa guwa mozungulira.

3Tsono apereke mafuta ake onse, mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo.

4Aperekenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi ochotsa ndi imso zija.

5Wansembe azitenthere pa guwa zonsezo, kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula.

6Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Aidyere pa malo oyera. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.

7Nsembe yopepesera kupalamula njofanafana ndi nsembe yopepesera machimo, ndipo nsembe ziŵiri zonsezo zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe wochita mwambo wopepesera machimo ndiye amene nyamayo ikhale yake.

8Ndipo wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake.

9Tsono chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni, kapena cha zonse zimene amakazinga mu mphika kapena m'chiwaya, zikhale za wansembe amene apereke zimenezo.

10Ndipo chopereka chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chouma, chikhale cha ana onse a Aroni. Anawo aigaŵane molingana.

Nsembe zachiyanjano

11“Lamulo la nsembe yachiyanjano imene aliyense angathe kupereka kwa Chauta ndi ili:

12akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta.

13Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo, abwere ndi mitanda ya buledi wotupitsa.

14Kenaka atengeko mtanda umodzi pa mtundu uliwonse wa buledi, kuti ukhale nsembe yopereka kwa Chauta. Mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe zachiyanjano.

15Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozerayo aidye pa tsiku lopereka nsembe yakeyo. Asaisungeko mpang'ono pomwe kufikira m'maŵa mwake.

16Koma nsembe yake ikakhala yoti waipereka moilumbirira kapena mwaufulu, aidye pa tsiku lomwe akuiperekalo, ndipo nyama yotsala aidye m'maŵa mwake.

17Koma nyama yotsalako kufikira tsiku lachitatu, aitenthe pa moto.

18Ngati munthu adya nyama ya nsembe yachiyanjano pa tsiku lachitatu, amene waiperekayo Mulungu sadzamulandira, ndipo nsembeyo sidzampindulira kanthu. Idzakhala chinthu chonyansa ndipo amene adzadye imeneyo adzakhala wopalamula.

19“Nyama imene ikhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, munthu asaidye, koma itenthedwe pa moto. Onse amene ali osaipitsidwa pa zachipembedzo angathe kudya nyama ya nsembe.

20Koma munthu woipitsidwa akadya nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.

21Ndipo wina aliyense akakhudza chinthu chonyansa pa zachipembedzo, kaya nchonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, tsono nadyako nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, munthuyo achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.”

22Chauta adauza Mose kuti,

23“Uza Aisraele kuti asadye mafuta ang'ombe, kapena ankhosa kapenanso ambuzi.

24Mafuta a nyama yofa yokha, ndi mafuta a nyama yojiwa ndi zilombo, angathe kuŵagwiritsa ntchito zina zilizonse, koma iwowo asadye.

25Pakuti munthu amene adya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Chauta kuti ikhale nsembe yotentha pamoto, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.

26Gen. 9.4; Lev. 17.10-14; 19.26; Deut. 12.16, 23; 15.23 Ndiponso kulikonse kumene akakhale, asadye magazi aliwonse, ambalame kapena anyama.

27Munthu aliyense wophwanya lamulo limeneli, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.”

28Chauta adauza Mose kuti,

29“Uza Aisraele kuti, ‘Munthu amene apereka nsembe yake yachiyanjano kwa Chauta, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Chauta. Pa nsembe yake yachiyanjanoyo

30atengeko ndi manja ake zigawo zoyenera kuzitentha, zopereka kwa Chauta, ndiye kuti mafuta ndi nganga yomwe. Tsono ngangayo aiweyule kuti ikhale chopereka choweyula kwa ine.

31Apo wansembe atenthe mafuta pa guwa, koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.

32Wansembe mumpatsenso ntchafu ya ku dzanja lamanja, kuti ikhale chopereka cha pa nsembe yanu yachiyanjano.

33Pakati pa ana a Aroni, wansembe amene apereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, ndiye adzalandire ntchafu ya ku dzanja lamanja ngati chigawo chake.

34Choncho nganga yopereka moweyula manjayo, pamodzi ndi ntchafu yoperekayo, ndikuzichotsa zonsezo kwa Aisraele. Ndikuzichotsa pa nsembe zao zachiyanjano, ndipo ndikuzipereka kwa wansembeyo Aroni ndi kwa ana ake, kuti zikhale chigawo chao nthaŵi zonse.

35Chimenecho ndicho chigawo cha Aroni ndi cha ana ake, chotapa pa zopereka kwa Chauta zoyenera kutentha pa moto, chimene chidapatulidwa kuti chikhale chigawo chao, pa tsiku limene iwo adaperekedwa kuti akhale ansembe otumikira Chauta.

36Chauta ndiye amene adalamula Aisraele kuti azipereka zimenezi kwa ansembe, pa tsiku limene adadzozedwa. Zimenezo ndizo chigawo chao nthaŵi zonse pa mibadwo yao yonse.’ ”

37Ameneŵa ndiwo malamulo a nsembe zonsezi: yopsereza, ya chakudya, yopepesera machimo, yopepesera kupalamula, yakudzoza, ndiponso yachiyanjano.

38Malamulo ameneŵa ndi amene Chauta adapereka kwa Mose pa phiri lija la Sinai, pa tsiku limene adalamula Aisraele kuti abwere ndi nsembe zao kwa Chauta, ku chipululu cha Sinai chija.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help