1 Pet. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za moyo watsopano

1Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo.

2Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu.

3Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.

4Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata.

5Koma iwo adzayenera kufotokoza okha mlandu wao kwa Mulungu amene ali wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

6Nchifukwa chake Uthenga Wabwino udalalikidwa ndi kwa amene adafa omwe, kuti ngakhale adaweruzidwa m'thupi monga anthu, komabe mu mzimu akhale ndi moyo monga Mulungu.

Akhristu agwiritse ntchito mphatso za Mulungu

7Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.

8Miy. 10.12; Tob. 12.9Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

9Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula.

10Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

11Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Kumva zoŵaŵa chifukwa cha chikhristu

12Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo.

13Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.

14Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.

15Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.

16Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo.

17Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani?

18Miy. 11.31 Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?”

19Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help