Aef. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ana ndi makolo

1 Akol. 3.20 Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.

2Eks. 20.12; Deut. 5.16 Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.

3Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

4 Akol. 3.21 Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Za akapolo ndi ambuye ao

5 Akol. 3.22-25 Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe.

6Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna.

7Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe.

8Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

9 Akol. 4.1; Deut. 10.17; Akol. 3.25 Inu ambuye, muziŵachitiranso chimodzimodzi akapolo anu, ndipo muleke zoŵaopseza. Paja mukudziŵa kuti iwoŵa ndi inuyo, nonse muli ndi Mbuye wanu Kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.

Za zida zankhondo zimene Mulungu amapatsa anthu ake

10Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

11Lun. 5.17Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

12Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

13Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.

14 Lun. 5.18-23 Yes. 11.5; Yes. 59.17 Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.

15Yes. 52.7Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.

16Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.

17Yes. 59.17Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.

18Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.

19Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.

20Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.

Mau otsiriza

21 Ntc. 20.4; 2Tim. 4.12 Akol. 4.7, 8 Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.

22Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.

23Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.

24Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help