1Yesu adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika ndi mphamvu.”
Za kusinthika kwa maonekedwe a Yesu(Mt. 17.1-13; Lk. 9.28-36)2 2Pet. 1.17, 18 Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona.
3Zovala zake zidasanduka zoŵala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m'mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano.
4Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Eliya ndi Mose, akukambirana ndi Yesu.
5Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.”
6Ankatero chifukwa chosoŵa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu.
7Mt. 3.17; Mk. 1.11; Lk. 3.22Tsono padafika mtambo, nuŵaphimba, ndipo mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.”?
8Mwadzidzidzi ophunzirawo poyang'anayang'ana, adangoona kuti palibenso wina amene anali nawo pamenepo, koma Yesu yekha.
9Pamene ankatsika phirilo, Yesu adaŵaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.
10Iwo adasungadi chinsinsichi, koma ankafunsana okhaokha kuti, “Kodi kuuka kwa akufa akunena Yesuku ndiye kuti chiyani?”
11Mal. 4.5; Mt. 11.14 Tsono adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?”
12Mphu. 48.10 Yesu adaŵayankha kuti, “Zoonadi, Eliya adzayambadi wabwera, kuti adzakonzenso zonse. Komabe bwanji Malembo amanena kuti Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri ndi kunyozedwa?
13Ine ndikukuuzani kuti Eliya adafikadi, ndipo anthu adamchita zonse zomwe iwo ankafuna, monga momwe Malembo adaanenera za iye.”
Yesu achiritsa mnyamata wogwidwa ndi mzimu woipa(Mt. 17.14-20; Lk. 9.37-43)14Pamene Yesu ndi ophunzira atatuwo adabwerera kwa ophunzira ena aja, adapeza chikhamu chachikulu cha anthu chitaŵazinga. Aphunzitsi a Malamulo ankatsutsana ndi ophunzirawo.
15Pamene anthu onsewo adaona Yesu, adadabwa kwambiri, ndipo adamthamangira kudzamlonjera.
16Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi mukutsutsana zotani?”
17Mmodzi mwa anthuwo adayankha kuti, “Aphunzitsi, ine ndinabwera ndi mwana wanga wamwamuna kuti ndidzampereke kwa Inu, chifukwa adaloŵedwa ndi mzimu woipa womuletsa kulankhula.
18Umati ukangomugwira, umamgwetsa pansi, mwanayo nkumangoti thovu tututu kukamwa, namakukuta mano, mpaka thupi gwagwagwa kuuma. Ndiye ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.”
19Apo Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.”
20Adabwera nayedi. Mzimu woipa uja utangoona Yesu, nthaŵi yomweyo wayamba kumzunguza mwamphamvu mnyamata uja, mpaka iye pansi khu, nkumangovimvinizika, thovu lili tututu kukamwa.
21Yesu adafunsa bambo wake uja kuti, “Kodi zimenezi zidamuyamba liti?” Bambo wakeyo adati, “Zidamuyamba ali mwana ndithu.
22Mzimu umenewu wakhala ukumugwetsa kaŵirikaŵiri, mwina amagwa pa moto, mwina m'madzi, kufuna kumupha. Koma ngati Inu mungathe kuchitapo kanthu, chonde tatichitirani chifundo, mutithandize.”
23Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”
24Pomwepo bambo wa mwana uja adanena mokweza mau kuti, “Ndikukhulupirira, koma mpang'ono chabe. Thandizeni kuti ndikhulupirire kwenikweni.”
25Pamene Yesu adaona kuti chikhamu cha anthu chija chayamba kupanikizana pamenepo, adazazira mzimu woipawo, adati, “Iwe mzimu woletsa kulankhula ndi kumva, ndikukulamula kuti utuluke mwa mwanayu, ndipo usadzaloŵenso mwa iye.”
26Mzimuwo udafuula numzunguza mwamphamvu mwana uja, kenaka nkutuluka. Mwanayo adangoti zii ngati wafa, mpaka ambiri nkumati, “Watsirizika basi!”
27Koma Yesu adamugwira dzanja namdzutsa, mwanayo nkuimirira.
28Yesu atakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa ali paokha, kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?”
29Yesu adayankha kuti, “Mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera mpamene mungautulutse.”
Yesu aneneratunso za kufa ndi kuuka kwake(Mt. 17.22-23; Lk. 9.43-45)30Atachoka kumeneko, Yesu ndi ophunzira ake ankadutsa m'dziko la Galileya. Koma Iye sadafune kuti anthu adziŵe,
31chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.”
32Ophunzira ake sadamvetse mau ameneŵa, komabe ankaopa kumufunsa.
Wamkulu ndani?(Mt. 18.1-5; Lk. 9.46-48)33Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao. Ataloŵa m'nyumba, Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi panjira paja mumatsutsana zotani?”
34Lk. 22.24Ophunzirawo adangoti chete. Ndiye kuti zimene ankatsutsana panjirapo zinali zakuti wamkulu ndani pakati pao.
35Mt. 20.26, 27; 23.11; Mk. 10.43, 44; Lk. 22.26Yesu adakhala pansi, naŵaitana ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Ndipo adaŵauza kuti, “Ngati wina afuna kukhala wamkulu, adzisandutse wamng'ono, wotumikira onse.”
36Atatero adatenga mwana, namkhazika pakati pao nkumufungata, naŵauza kuti,
37Mt. 10.40; Lk. 10.16; Yoh. 13.20“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
Wosatsutsana nafe ngwogwirizana nafe(Lk. 9.49-50)38Yohane adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa chifukwa sayenda nafe.”
39Koma Yesu adati, “Musamletse ai, chifukwa munthu sangati atachita zamphamvu m'dzina langa, nthaŵi yomweyo nkundinyoza.
40Mt. 12.30; Lk. 11.23Chifukwa wosatsutsana nafe, ndi wogwirizana nafe ameneyo.
41Mt. 10.42Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Za zochimwitsa(Mt. 18.6-9; Lk. 17.1-2)42“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamuponya m'nyanja.
43Mt. 5.30Tsono ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukaloŵe uli ndi manja onse aŵiri ku Gehena, kwa moto wosazimika.”
[
44“Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”]
45“Ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku Gehena uli ndi miyendo yonse iŵiri.”
[
46“Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”]
47 Mt. 5.29 “Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse aŵiri.
48Yes. 66.24 Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.
49“Onse adzayeretsedwa ndi moto monga momwe nsembe imayeretsedwa ndi mchere.
50Mt. 5.13; Lk. 14.34, 35Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Moyo wanu ukhale ngati wothiridwa mchere, ndipo muzikhala ndi mtendere pakati panu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.