1Mabanja a Simeoni adalandiranso gawo lao, Yoswa atachita maere kachiŵiri. Dziko lake linali m'kati mwenimweni mwa dziko la mabanja a Yuda.
21Mbi. 4.28-33 Ndipo lidaphatikiza Beereseba, Molada,
3Hazara-Suwala, Bala, Ezemu,
4Elitoladi, Betuli, Horoma,
5Zikilagi, Betemari-Kaboti, Hazarasusa,
6Betelebaoti ndiponso Saruheni. Yonse inalipo mizinda 13, pamodzi ndi midzi yake.
7Panalinso Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani. Yonse inalipo mizinda inai, pamodzi ndi midzi yake.
8Imeneyi idaphatikizapo midzi yozungulira mizindayo, mpaka kukafika ku Baala-Tibere, ndiye kuti Rama wakumwera. Dziko limeneli ndi limene mabanja a fuko la Simeoni adalandira kukhala choloŵa chao.
9Gawo la Simeoni lidatapidwa ku gawo la Yuda, popeza kuti gawo la Yuda lidaali lalikulu kwambiri. Choncho choloŵa cha Simeoni chidatapidwa pa choloŵa cha Yuda.
Dziko la Zebuloni.10Mabanja a fuko la Zebuloni adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachitatu. Dziko limene adalandiralo lidakafika mpaka ku Saridi.
11Tsono malirewo adakwera naloŵa kuzambwe ku Mareyala, nakafika ku Debeseti ndi ku mtsinje wa kuvuma kwa Yokoneamu.
12Pa mbali ina ya Saridi adapita chakuvuma ku malire a Kisiloti-Tabori, mpaka ku Debarati, nakafika ku Yafiya.
13Kuchokera kumeneko, adabzola naloŵa chakuvuma kumapita ku Gatihefere ndi ku Etikazini, kuloŵa ku Neya njira yaku Rimoni.
14Kumpoto malire amenewo adapita molunjika ku Hanatoni, nakathera ku chigwa cha Ifutahele.
15Adaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Yonse inalipo mizinda 12, pamodzi ndi midzi yake.
16Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake inali m'dziko limene mabanja a fuko la Zebuloni adalandira ngati choloŵa chao.
Dziko la Isakara.17Mabanja a fuko la Isakara adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachinai.
18Gawo lao lidaphatikiza Yezireele, Kesuloti, Sunemu,
19Hafaraimu, Siyoni, Anaharati,
20Rabiti, Kisiyoni, Ebezi,
21Remeti, Enganimu, Enihada ndi Betepazezi.
22Malire amenewo adakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi ku Betesemesi, ndi kutsikira ku Yordani. Lidaphatikiza mizinda 16 pamodzi ndi midzi yake.
23Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Isakara adalandira ngati choloŵa chao.
Dziko la Asere.24Mabanja a fuko la Asere adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu.
25Gawo lake lidaphatikiza Helekati, Hali, Beteni, Akisafu,
26Alamumeleki, Amada ndi Misala. Kuzambwe malire adakafika ku Karimele ndi ku Sihori-Libinati.
27Adakhotera kuvuma naloŵera ku Betedagoni, nkukafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifitaele pa njira yakumpoto, kumapita ku Betemeke ndi ku Neiyeli. Adabzola kupita kumpoto mpaka kukafika ku Kabulu,
28Ebroni, Rehobu, Hamoni ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu.
29Tsono malirewo adakhotera ku Rama, nakafika mpaka ku Tiro, mzinda wozingidwa ndi linga. Pamenepo adakhoteranso ku Hosa, nkukatulukira ku nyanja, m'dera la Akizibu,
30Uma, Afeki ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda 22, pamodzi ndi midzi yake.
31Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Asere adalandira ngati choloŵa chao.
Dziko la Nafutali.32Mabanja a fuko la Nafutali adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chimodzi.
33Malire ake adayambira ku Helefe kuchokera ku mtengo wogudira wa ku Zaananimu. Adachokeranso ku Adami-Nekebu ndi ku Yabinele mpaka ku Lakumu, nakathera ku Yordani.
34Ndipo malirewo adakhotera kuzambwe ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko adaloŵera ku Hukoko, nakafika ku dziko la Zebuloni chakumwera, ndi ku dziko la Asere chakuzambwe, ndi ku mtsinje wa Yordani chakuvuma.
35Mizinda yamalinga inali iyi: Zidumu, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti,
36Adama, Rama, Hazori,
37Kedesi, Ederei, Enihazori,
38Yironi, Migidalele, Horemu, Betanati, ndi Betesemesi. Yonse inalipo mizinda 19, pamodzi ndi midzi yake.
39Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Nafutali adalandira ngati choloŵa chao.
Dziko la Dani.40Mabanja a fuko la Dani adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chiŵiri.
41Dziko laolo lidaphatikiza Zola, Esitaoli, Irisemesi,
42Saalabimu, Ayaloni, Itila,
43Eloni, Timna, Ekeroni,
44Eliteke, Gibetoni, Baalati,
45Yehudi, Beneberaki, Gatirimoni,
46Meyarikoni ndi Rakoni, ndiponso dziko loyang'anana ndi Yopa.
47Owe. 18.27-29 Pamene anthu a fuko la Dani adalandidwa dziko lao, adapita nakathira nkhondo Lesemu, nagonjetseratu ndi kuwononga adani onse. Tsono atatero, adalanda mzindawo, nakhazikika kumeneko. Ndipo adasintha dzina la mzindawo kuti likhale Dani, pakuti limeneli linali dzina la kholo lao Dani.
48Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yake, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Dani adalandira ngati choloŵa chao.
Agaŵa dziko kotsiriza.49Tsono Aisraele atatha kugaŵana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, adamgaŵirako Yoswa mwana wa Nuni dera lina la dzikolo kuti likhale choloŵa chake.
50Potsata zimene Chauta adalamula, adampatsako mzinda wa Timnati-Sera umene Yoswayo mwiniwake adaapempha, umene unali m'dziko la Efuremu lamapiri lija. Kumeneko ndiko kumene adamanga mzinda wake, nakhazikika komweko.
51Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, pamodzi ndi atsogoleri amabanja a Aisraele, ndiwo amene adagaŵa dziko limeneli zigawozigawo, pochita maere pamaso pa Chauta. Ndipo ankachita zimenezi ku Silo, ku chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano chija. Choncho adamaliza kuligaŵa dzikolo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.