Lk. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu atuma anthu 72

1Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko.

2 pa njira.

5Kunyumba kulikonse kumene mukaloŵe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m'nyumba muno.’

6Ngati m'nyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu.

7 koposa polanga mudzi umenewo.

Za tsoka la midzi yosatembenuka mtima(Mt. 11.20-24)

13 Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.

14Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu.

15 kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.”

16 Mt. 10.40; Mk. 9.37; Lk. 9.48; Yoh. 13.20 Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”

Otumidwa aja abwerako

17Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.”

18Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba.

19Mas. 91.13Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.

20Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”

Yesu akondwera(Mt. 11.25-27; 13.16-17)

21Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.

22 Yoh. 3.35; Yoh. 10.15 “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.”

23Pambuyo pake Yesu adatembenukira ophunzira ake, naŵauza iwo okha kuti, “Ngodala maso amene akuwona zimene mukuwonazi.

24Kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu ambiri adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.”

Fanizo la Msamariya wachifundo

25 Mt. 22.35-40; Mk. 12.28-34 Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”

26Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?”

27Deut. 6.5; Lev. 19.18 Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

28Lev. 18.5Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”

29Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?”

30Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.

31“Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala.

32Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala.

332Mbi. 28.15Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni.

34Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.

35M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”

36Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?”

37Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”

Yesu akacheza kwa Marita ndi Maria

38 Yoh. 11.1 Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adaloŵa m'mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake.

39Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake.

40Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng'ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.”

41Ambuye adati, “Iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri,

42koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help