1Nchifukwa chake tsono, zimene tidamva, tizizisamala kwambiri, kuwopa kuti pang'ono ndi pang'ono tingazitaye.
2Mau amene Mulungu adalankhula kudzera mwa angelo anali okhazikika ndithu, kotero kuti aliyense amene sadaŵamvere kapena amene adaŵanyoza, adalangidwa monga momwe kudamuyenerera.
3Nanga ife tingapulumuke bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiwo amene adalankhula poyamba za chipulumutsochi, kenaka amene adamva mau aowo, adatitsimikizira kuti ndi oona.
4Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.
Za mtsogoleri wa chipulumutsocho5Tikamanena za dziko limene lilikudza, si angelo amene Mulungu adaŵapatsa ulamuliro pa dzikolo.
6Mas. 8.4-6 Koma pena pake wina adanenetsa m'Malembo kuti,
“Kodi munthu nchiyani, kuti muzimkumbukira,
mwana wa munthu nchiyani, kuti muzimsamala?
7Kanthaŵi pang'ono mudamsandutsa wochepera kwa angelo.
Mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu,
8ndipo mudampatsa ulamuliro pa zinthu zonse.”
Tsono ngati Mulungu adapatsa munthu ulamuliro pa zinthu zonse, palibe kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Komabe m'mene zinthu ziliri tsopano sitikuwona kuti zonse zakhaladi mu ulamuliro wakewo.
9Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
10Paja Mulungu amene ndi Mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zoŵaŵa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro woŵatsogolera ku chipulumutso.
11Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi. Nchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuŵatchula abale ake,
12Mas. 22.22 ponena mau akuti,
“Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu.
Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.”
13 Yes. 8.17; Yes. 8.18 Amanenanso kuti,
“Ndidzakhulupirira Mulungu.”
Penanso amanena kuti,
“Ine ndili pano,
pamodzi ndi ana amene Mulungu adandipatsa.”
14Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa.
15Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.
16Yes. 41.8, 9 Paja nchodziŵikiratu kuti sadatekeseke ndi angelo ai koma ndi zidzukulu za Abrahamu.
17Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu.
18Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.