Yes. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzatchinjiriza Yerusalemu

1Tsoka kwa amene amapita ku Ejipito

kukapempha chithandizo.

Iwo amadalira akavalo,

ndipo amakhulupirira kuchuluka

kwa magaleta ao ankhondo,

ndiponso mphamvu za asilikali ao

okwera pa akavalo.

Koma sakhulupirira Woyera uja wa Israele,

kapena kupempha chithandizo kwa Chauta.

2Komabe Chautayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga.

Sabweza zimene wanena, adzalimbana ndi anthu oipa

ndiponso ndi anthu amene amathandiza oipawo.

3Aejipito ndi anthu chabe, si milungu ai.

Akavalo ao si mizimu, koma ndi nyama chabe.

Chauta akachitapo kanthu,

opereka chithandizo adzaphunthwa,

olandira chithandizocho adzagwa,

ndipo onsewo adzathera limodzi.

4Chauta adandiwuza kuti,

“Monga momwe mkango kapena msona wa mkango

umabangulira utagwira nyama,

ndipo abusa sangaupirikitse,

ngakhale auwopseze ndi kufuula chotani,

motero palibe chimene chingaletse

Chauta Wamphamvuzonse kutchinjiriza

Phiri la Ziyoni ndi gomo lake.

5Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake,

Chauta Wamphamvuzonse

adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu.

Adzauteteza ndi kuupulumutsa,

adzausiya pambali ndi kuuwombola.”

6Inu Aisraele, bwererani kwa Iye amene mudampandukira kwakukulu.

7Pajatu tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu asiliva ndi agolide, amene mudapanga ndi manja anu auchimo.

8“Aasiriya adzaonongedwa pa nkhondo,

osati ndi mphamvu ya munthu.

Adzaonongedwa ndi lupanga,

lupanga lake osati la munthu.

Adzathaŵa ku nkhondo,

ndipo anyamata ao adzakhala akapolo.

9Mfumu yao idzathaŵa ndi mantha,

ndipo atsogoleri ake ankhondo

adzabalalika mwamantha kwambiri,

kotero kuti adzasiya mbendera zao zankhondo,”

akutero Chauta amene moto wake uli ku Ziyoni,

ndipo ching'anjo chake chili ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help