Mla. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu onse mathero ao ndamodzi

1Zonse ndanenazi ndidazilingalirapo, ndipo ndidatsimikiza kuti anthu ochita chilungamo ndi anthu anzeru ali m'manja mwa Mulungu pamodzi ndi ntchito zao zomwe. Koma palibe munthu angadziŵe zimene zili m'tsogolo mwake, ngakhale zikhale za chikondi, kapena za chidani.

2Anthu onse zimene zidzaŵaonekere nzimodzimodzi, ochita chifuniro cha Mulungu ndi okana omwe, abwino ndi oipa, osamala zachipembedzo ndi osasamala omwe, opereka nsembe ndi osapereka omwe. Wabwino amafanafana ndi woipa. Wochita malumbiro amafanafana ndi woopa kulumbira.

3Chimene chili choipa kwambiri mwa zonse zochitika pansi pano ndi ichi chakuti tsoka limodzimodzi limagwera onse. Chinanso nchakuti mitima ya anthu njodzaza ndi zoipa. M'mitima mwao mumadzaza ndi zamisala pamene ali moyo, pambuyo pake kwao nkufa ndithu.

4Komabe amene ali ndi moyo ali nacho chikhulupiriro. Paja akuti ndiponi galu wamoyo kuposa mkango wakufa.

5Amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa kanthu, ndipo alibe mphotho inanso yoonjezera. Palibe ndi mmodzi yemwe woŵakumbukira.

6Chikondi chao, chidani chao ndi nsanje yao, zonse zidatha kale. Ndipo pa zonse zochitika pansi pano sadzalandirako kanthu konse mpakampaka.

Uzisangalala pamene ungathe

7Ndiye iwe usaope, uzidya chakudya chako mokondwa, uzimwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti Mulungu wavomereza kale zochita zakozo.

8Uzivala zovala zoyera nthaŵi zonse, uzidzola mafuta nthaŵi zonse.

9Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano.

10Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.

Mwai umagwera aliyense

11Ndidaonanso pansi pano kuti opambana pa kuthamanga si aliŵiro okhaokha, opambana pa nkhondo si amphamvu okhaokha, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru okhaokha. Olemera si odziŵa zambiri okhaokha, ndipo si anthu aluso okhaokha amene anzao amaŵakomera mtima. Onsewo mwai umangoŵagwera pa nthaŵi yake.

12Kungoti munthu saidziŵa nthaŵi yake. Monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, monga momwenso mbalame zimakodwera mu msampha, anthunso nchimodzimodzi. Amachita ngati kukodwa mu msampha pa nthaŵi yoipa, pamene tsoka laŵagwera mwadzidzidzi.

Nzeru ndiye zili patsogolo

13Pansi pano ndidaonanso chinthu china chokhudza nzeru, ndipo ine ndidachiwona kuti nchinthu chachikulu.

14Panali mzinda waung'ono, m'mene munali anthu oŵerengeka. Tsono padafika mfumu yamphamvu kudzauthira nkhondo mzindawo, nkuuzinga ndi zithando zankhondo.

15Koma mumzindamo munali munthu wina wosauka koma wanzeru. Munthu ameneyo adaupulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Komabe panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkumbukira wosaukayo.

16Ndiye ine ndikuti nzeru nzabwino ndithu kupambana mphamvu, ngakhale kuti anthu sazimvera nzeru za munthu wosauka, ndipo za mau ake salabadako nkomwe.

17Mau a munthu wanzeru, olankhula mofatsa, ndi abwino kupambana kufuula kwa mfumu pa gulu la zitsiru.

18Nzeru nzabwino kupambana zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi amatha kuwononga zabwino zambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help