1Chauta adandiwuza kuti
2ndikalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu mau ake akuti,
“Ndikukumbukira m'mene munkakhulupirikira
pa unyamata wanu,
m'mene poyamba paja munkandikondera
monga amachitira mkwati wamkazi.
Mudanditsata m'chipululu,
m'dziko losabzalamo kanthu.
3Iwe Israele udaali wopatulika wa Chauta.
Udaali ngati chipatso chake choundukula.
Ndidaika zoŵaŵa ndi mavuto aakulu,
pa onse amene adakuzunza,
ndipo tsoka linkaŵagwera,” akutero Chauta.
4Inu zidzukulu za Yakobe, mabanja onse a Israele, mverani mau a Chauta.
5Iye akukufunsani kuti,
“Kodi makolo anu adandipeza ncholakwa chanji kuti andithaŵe?
Adatsata milungu yachabechabe,
iwonso nkusanduka achabechabe.
6Sadalabadeko za Ine Chauta,
ngakhale ndine amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Aejipito,
ndi kuŵatsogolera m'chipululu,
m'dziko louma ndi lokumbikakumbika,
m'dziko lachilala ndi la mdima wandiweyani,
m'dziko limene munthu sadutsamo,
kumene sikukhala munthu konse.
7Ndidakufikitsani ku dziko lachonde
kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.
Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa,
dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.
8Nawonso ansembe sadafunse kuti,
‘Chauta ali kuti?’
Akatswiri a malamulo sadandidziŵe.
Olamulira adandipandukira.
Aneneri ankalosa m'dzina la Baala,
ndipo ankatsata milungu yachabechabe.
Chauta aŵaimba mlandu anthu ake9“Tsono ndidzakuimbanibe mlandu,”
akuterotu Chauta.
“Ndidzaimbanso mlandu zidzukulu zanu.
10Pitani chakuzambwe, ku chilumba cha Kitimu, mukaone,
tumani anthu chakuvuma, ku Kedara, akafufuze.
Mudzaona kuti zoterezi sizidachitikepo nkale lonse.
11Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse
umene udasinthapo milungu yake,
ngakhale kuti si milungu konse?
Komabe anthu anga asinthitsa Mulungu wao
waulemerero ndi milungu yachabechabe.
12Inu maiko akumwamba, dabwa nazoni zimenezi,
njenjemerani ndi mantha,
akuterotu Chauta.
13Anthu anga achita machimo aŵiri:
andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo,
adzikumbira okha zitsime,
zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi.
Zotsatira za kusakhulupirika kwa Aisraele14“Israele si kapolotu ai,
sadabadwire mu ukapolo.
Nanga chifukwa chiyani amuwononga chotere?
15Anthu a mitundu ina ambangulira
ndi kumuwopsa ngati mikango.
Dziko lake alisandutsa chipululu.
Mizinda yake adaiwononga, idasanduka mabwinja.
16Aejipito a ku Memfisi ndi a ku Tapanesi
akuphwanyani mitu.
17Zimenezi zakuwonekerani
chifukwa mudasiya Chauta, Mulungu wanu,
pamene Iye adakuikani pa njira yabwino.
18Nanga tsopano mudzapindulanji mukadzapita ku Ejipito,
kukamwa madzi a m'Nailo?
Mudzapeza phindu lanji mukadzapita ku Asiriya
kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe:
poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu.
Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine,
Chauta, Mulungu wanu.
Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,”
akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Aisraele akana kupembedza Chauta20“Kuyambira masiku amakedzana inu mudathyola goli lanu
ndi kudula nsinga zanu.
Mudati, ‘Sitidzakutumikirani!’
Ndithu inu mwakhala ngati mkazi wadama,
mukupembedza milungu ina pochita zadama
pa phiri lililonse
ndiponso pansi pa mtengo wogudira uliwonse.
21Komabe ndidaakuwoka iwe Israele
ngati mtengo wa mphesa wosankhidwa,
udaali mpesa wabwino kwambiri.
Nanga wasanduka bwanji mpesa wachabechabe,
wonga wakutchire?
22Ngakhale usambire soda,
ngakhale usambire sopo wambiri,
kuthimbirira kwa tchimo lako
kumaonekabe pamaso panga,”
akuterotu Ambuye Chauta.
23“Uneneranji kuti, ‘Ine sindidadziipitse,
sindidatsate Baala?’
Kumbukira m'mene udachimwira m'chigwamo,
zindikira zimene wachita.
Wakhala ngati ngamira yaikazi,
yothamanga uku ndi uku.
24Wakhala ngati mbidzi yaikazi yozoloŵera m'chipululu,
yonka nipunika pa nthaŵi yake yachisika.
Kodi angailetse chilakolako chakecho ndani?
Mphongo iliyonse yoikhumba sidzavutika,
idzaipeza pa nthaŵi yakeyo.
25Iwe Israele, lekatu, nsapato zingakuthere ku phazi,
kukhosi kwako kungaume ndi ludzu potsatira milungu ina.
Koma iwe ukuti,
‘Ai toto, sindingathe kuchitira mwina,
ndimakonda milungu yachilendoyi,
sindingaleke kuitsata.’
Israele ayenera kulangidwa26“Banja la Israele lidzachita manyazi,
monga momwe mbala imachitira manyazi akaigwira.
Aisraele, mafumu ao ndi akalonga ao,
ansembe ao ndi aneneri ao,
onsewo adzachita manyazi.
27Amauza mtengo kuti ‘Iwe ndiwe bambo wathu,’
amauza mwala kuti ‘Iwe ndiwe amene udatibala.’
Koma Ine amandifulatira,
m'malo motembenukira kwa Ine.
Tsono akakhala pa mavuto amati,
‘Dzambatukani, mutithandize.’
28Nanga milungu yanu ili kuti,
milungu ija mudadzipangira ija?
Idzambatuketu, ngati ingathe kukupulumutsani
pa nthaŵi yanu ya mavuto.
Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri,
kuchuluka kwake monga momwe iliri mizinda yanu.”
29Chauta akuti,
“Kodi mukundiimbiranji mlandu?
Nonsenu mwandipandukira.
30Ndidalanga ana anu popanda phindu,
sadaphunzirepo nkanthu komwe.
Monga mkango wolusa mudapha aneneri anu ndi lupanga.”
31Inu anthu amakono, imvani mau a Chauta.
“Kodi ndakhala ngati chipululu kwa Israele,
kapena ngati dziko la mdima wandiweyani?
Chifukwa chiyani tsono anthu anga akunena kuti,
‘Ndife mfulu,
sitidzabweranso kwa Inu?’
32Kodi namwali amaiŵala zokongoletsera zake,
kapena mkwati kuiŵala zovala zake zaukwati?
Komabe anthu anga andiiŵala Ine masiku osaŵerengeka.
33“Mumadziŵa bwino njira zopezera zibwenzi zam'seri.
Ngakhale akazi oipa kwambiri omwe mumaŵaphunzitsa ndinu.
34Zovala zanu zili psu
ndi magazi a anthu osauka osachimwa.
Anthuwo simudaŵapeze nathyola nyumba.
Komabe, ngakhale zinthu zili choncho,
35inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,
mkwiyo wa Chauta wapola tsopano!’
Ine ndidzakuimbanibe mlandu
chifukwa chonena kuti simudachimwe.
36Bwanji mukudzipeputsa nokha
posinthasintha njira zanu!
Ejipito adzakugwiritsani mwala
monga muja adakuchititsirani manyazi Aasiriya.
37Mudzatuluka kumeneko
aliyense atagwirira manja ku mutu.
Ine Chauta ndidaŵakana amene inu mumagonerapo,
ndipo anthuwo sadzakuthandizani mpang'ono pomwe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.