2 Sam. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide akhululukira Abisalomu.

1Yowabu, mwana wa Zeruya, adaadziŵa kuti mtima wa mfumu uli pa Abisalomu.

2Tsono adatuma anthu ku Tekowa kukatengako mkazi wanzeru kumeneko. Adauza mkaziyo kuti, “Ukhale ngati mfedwa, uvale zovala zaumasiye. Usadzole mafuta, koma ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri.

3Ukatero upite kwa mfumu, ukalankhule nayo izi, izi.” Choncho Yowabu adauza mkaziyo mau oti akanene.

4Mkazi wa ku Tekowayo atafika kwa mfumu, adadzigwetsa pansi, nalambira mfumu, ndipo adati, “Pepani amfumu, thandizeni.”

5Mfumuyo idamufunsa kuti, “Chikukuvutani nchiyani, mai?” Mkaziyo adayankha kuti, “Ha! Munthune ndine mkazi wamasiye. Mwamuna wanga adafa.

6Ndiye ine mdzakazi wanu ndinali ndi ana aamuna aŵiri, anawo ankamenyana kuminda. Panalibe wina aliyense woti aŵaleretse, choncho wina adakantha mnzake mpaka kumupha.

7Tsono banja lonse landiwukira ine mdzakazi wanu, akunena kuti, ‘Utipatse mwana wako amene adapha mbale wake, kuti ife timuphe chifukwa cha mbale wake amene iye adaphayo.’ Motero anthuwo adzaononganso mloŵachuma. Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika, pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.”

8Apo mfumu idauza mkazi uja kuti, “Mai, pitani kunyumba kwanu, ndichitapo kanthu ineyo pa nkhaniyi.”

9Mkazi wa ku Tekowa uja adauza mfumu kuti, “Inu amfumu, mlandu umenewu ugwere ine ndi banja la bambo wanga, inuyo mukhale osalakwa pamodzi ndi banja lanu lonse.”

10Apo mfumu idati, “Ngati wina aliyense akunenerani kanthu kena kalikonse, mubwere naye kwa ine, ndipo sadzakuvutitsaninso.”

11Tsono mkazi uja adanena kuti, “Chonde, amfumu mupemphe kwa Chauta Mulungu wanu, kuti wolipsira imfa ija asaphenso wina, kuti choncho mwana wanga asaonongeke.” Davide adati, “Pali Chauta wamoyo, mwana wanu sadzapwetekedwa mpang'ono pomwe.”

12Tsono mkaziyo adati, “Chonde, mulole kuti ine mdzakazi wanu ndilankhule mau ena kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumuyo idamuuza kuti, “Lankhulani, mai.”

13Apo mkazi uja adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani nanga mwaganiza zoŵachita zinthu zotere anthu a Mulungu? Chifukwatu pochita zimenezi inu amfumu mwadziimba mlandu nokha, malinga nkuti simudaitanitse wopirikitsidwa uja kuti abwererenso kwao.

14Paja madzi akatayika saoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike, tsono amakonza njira yakuti wopirikitsidwa asakhale wotayikiratu chonse.

15Ndiye ine ndafika kuti ndidzalankhule ndi inu amfumu. Mwina mwake mungathe kudzachita zimene mdzakazi wanune ndikupempha.

16Ndimaganiza kuti inu amfumu mutazimva, mudzandipulumutsa kwa munthu amene afuna kundiwononga ine pamodzi ndi mwana wanga, potero nkutichotsa pa kadziko kathu kamene adatipatsa Mulungu.

172Sam. 19.27Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.”

18Apo mfumu idamuyankha mkaziyo kuti, “Musandibisire kanthu kalikonse pa zimene ndikufunseni.” Mkazi uja adati, “Ai ndithu, mbuyanga mfumu sindikubisirani.”

19Tsono mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi zimenezi Yowabu sakuzidziŵa?” Mkaziyo adayankha kuti, “Pali inu nomwe, mbuyanga mfumu, palibe munthu amene angathe kupewa kuyankha chilichonse chimene inu mwafunsa. Kunena zoona, mtumiki wanu Yowabu ndiye amene adandiwuza kuti ndichite zimenezi. Iyeyo ndiye adandiwuza ine mdzakazi wanu mau onseŵa.

20Mtumiki wanu Yowabu adachita zimenezi kuti asinthe mayendedwe ake a zinthu. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru zonga za mngelo wa Mulungu, mutha kudziŵa zinthu zonse za pa dziko lapansi.”

21Pambuyo pake mfumu idauza Yowabu kuti, “Chabwino tsono, ndavomera kuti zimenezi zichitike. Pita, kamtenge mnyamata uja Abisalomu.”

22Yowabu adaŵerama pansi, adalambira mfumu, naithokoza. Tsono adati, “Tsopano ndadziŵa kuti inu mbuyanga mfumu mwandikomera mtima, chifukwa mwavomera pempho langali.”

23Choncho Yowabu adanyamuka, adapita ku Gesuri, nakatenga Abisalomu, nkubwera naye ku Yerusalemu.

24Komabe mfumu idati, “Akhale payekha m'nyumba yakeyake. Asabwere pamaso panga.” Motero Abisalomu adakhala pa yekha m'nyumba yakeyake, osafika pamaso pa mfumu.

Davide ayanjananso ndi Abisalomu.

25M'dziko lonse la Israele panalibe munthu wina aliyense wokongola ndi wochititsa kaso ngati Abisalomu. Kuyambira kumapazi mpaka kumutu analibe chilema chilichonse.

26Chaka chilichonse ankameta tsitsi lake, chifukwa linkamlemera kwambiri. Ankati akalimeta Abisalomuyo, naliyesa pa sikelo tsitsilo, linkalemera makilogramu aŵiri, potsata muyeso wa mfumu.

27Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu, ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Iyeyu anali mkazi wokongola.

28Choncho Abisalomu adakhala zaka ziŵiri zathunthu mu Yerusalemu, osaonekera kwa mfumu.

29Tsiku lina adatumiza mau kwa Yowabu opempha kuti amtume kwa mfumu. Koma Yowabu sadafike. Abisalomu adatumizanso mau kachiŵiri, koma Yowabu osafika ndithu.

30Pamenepo Abisalomu adauza atumiki ake kuti, “Munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo ali ndi barele m'menemo. Pitani kautentheni.” Pompo atumiki a Abisalomu adapita kukautentha mundawo.

31Tsono Yowabu adanyamuka kupita kunyumba kwa Abisalomu, nakamufunsa kuti, “Bwanji atumiki ako atentha munda wanga?”

32Abisalomu adayankha kuti, “Taona, ine ndinkatumiza mau kwa iwe kuti ndidzakutume kwa mfumu kukaifunsa kuti chifukwa chiyani ndidachoka ku Gesuri kubwera kuno? Kunali kwabwino koposa kuti ine ndizikhalabe konkuja.” Abisalomu adapitirira nati, “Ndipite basi kwa mfumu. Ngati ndili ndi cholakwa, mfumuyo ikandiphe.”

33Apo Yowabu adapita kwa mfumu, nakakambira mfumuyo zimenezo. Tsono mfumu idaitana Abisalomu. Iye adabwera kwa mfumu, nadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Ndipo mfumuyo idamlandira bwino pakumumpsompsona.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help