Lev. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zonyansa zotuluka m'thupi

1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

2“Muuze Aisraele kuti: Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zimenezo nzonyansa ndithu.

3Lamulo lake lokhudza za kudziipitsa ndi zonyansa zotuluka ku maliseche a munthu nali: malisechewo akamatulutsabe mafinya, kaya aleka, munthuyo ndi woipitsidwa ndithu.

4Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonepo, lidzakhala loipitsidwa. Chinthu chilichonse chimene akhalepo, chidzakhala choipitsidwa.

5Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake, ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

6Munthu amene akhale pa chinthu chilichonse chimene wotulutsa mafinyayo adakhalapo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

7Aliyense wokhudza thupi la munthu wotulutsa mafinyayo, achape zovala zake ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

8Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu mnzake amene ali wosaipitsidwa, mnzakeyo achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

9Ndipo chokhalira chilichonse chapakavalo, chimene munthu wotulutsa mafinya uja adakhalapo, chidzakhala choipitsidwa.

10Aliyense amene akhudze chinthu chilichonse chimene munthuyo adakhalapo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense amene achinyamule, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

11Aliyense amene munthu wotulutsa mafinyayo amkhudze asanasambe m'manja, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

12Chiŵiya chadothi chimene munthu wotulutsa mafinyayo akhudze, achiphwanye, ndipo chiŵiya chilichonse chamtengo achitsuke m'madzi.

13“Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri a kuyeretsedwa kwake, kenaka achape zovala zake, asambe pa kasupe, ndipo adzakhala woyeretsedwa.

14Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndi kubwera nazo pamaso pa Chauta pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo azipereke kwa wansembe.

15Wansembeyo apereke zimenezo, kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ina ikhale nsembe yopsereza. Pamenepo wansembeyo ndiye kuti wachita mwambo wopepesera pamaso pa Chauta machimo a munthu wotulutsa mafinya uja.

16“Mwamuna akataya pansi mbeu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

17Chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse pomwe pagwera mbeu yaumunapo achitsuke, koma zikhalabe zoipitsidwa mpaka madzulo.

18Mwamuna akataya mbeu yake pogona ndi mkazi, onse aŵiriwo asambe, koma akhalabe oipitsidwa mpaka madzulo.

19“Mkazi akakhala wosamba, ndipo ikakhala nthaŵi yeniyeni yakusamba, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, aliyense amene amkhudze akhala woipitsidwa mpaka madzulo.

20Ndipo chilichonse chimene mkaziyo agonere ali woipitsidwabe, chikhala choipitsidwa. Chinthu china chilichonse chimene akhalire chikhala choipitsidwa.

21Aliyense wokhudza bedi la mkaziyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhala woipitsidwa mpaka madzulo.

22Aliyense wokhudza chimene mkaziyo amakhalapo, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

23Kaya chinthucho chikhale bedi kapena chinthu china chilichonse chimene mkaziyo amakhalapo, munthu akachikhudza, akhala woipitsidwa mpaka madzulo.

24Mwamuna aliyense akagona ndi mkazi amene akusambabe, mwamunayo akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo bedi lililonse limene mwamunayo agonepo likhala loipitsidwa.

25“Mkazi akataya magazi masiku ambiri osakhala nthaŵi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira pa nthaŵi yake ya kusamba, masiku onsewo mkaziyo ali wotaya magazi ndi woipitsidwa, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba.

26Bedi lililonse limene mkaziyo agonepo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, lidzakhala loipitsidwa. Ndipo zonse zimene amakhalirapo zikhala zoipitsidwa, monga momwe zimakhalira zoipitsidwa pamene ali wosamba pa nthaŵi yake.

27Aliyense wokhudza zimenezi akhala woipitsidwa. Tsono achape zovala zake ndi kusamba thupi lonse, koma akhala woipitsidwabe mpaka madzulo.

28Atatha matenda a kusamba kwakeko, mkazi aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake akhala woyeretsedwa.

29Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano.

30Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo ina ikhale nsembe yopsereza. Akatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Chauta, chifuwa cha matenda ake osamba aja.

31“Choncho mudzaŵayeretsa Aisraele m'kuipitsidwa kwao, kuti angafe chifukwa chochita tchimo la kudetsa chihema changa, chimene chili pakati pao.”

32Lamulo limeneli ndi la mwamuna amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya m'thupi mwake, ndiponso la amene ataya pansi mbeu yake yaumuna, imene imamsandutsa woipitsidwa.

33Lamulo limenelinso ndi la mkazi amene ali ndi matenda osamba. Lamuloli ndi la aliyense, mwamuna kapena mkazi, amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya kumaliseche kwake, ndiponso la mwamuna amene agona ndi mkazi woipitsidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help